Numeri 11:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Kodi Ndine amene ndinatenga pathupi pa anthu onsewa? Kodi ndinawabala ndine? Bwanji mukundiwuza kuti ndiwanyamule mʼmanja mwanga, monga momwe mlezi amanyamulira kamwana, kupita nawo ku malo omwe munalonjeza ndi lumbiro kwa makolo awo? Onani mutuwoBuku Lopatulika12 Kodi ndinaima nao anthu awa onse? Kodi ndinawabala, kuti munene nane, Uwayangate ngati mlezi afukata khanda, kunka nao ku dzikolo mudalumbirira makolo ao? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Kodi ndinaima nao anthu awa onse? Kodi ndinawabala, kuti munene nane, Uwayangate ngati mlezi afukata khanda, kunka nao ku dzikolo mudalumbirira makolo ao? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Kodi ndidaatenga pathupi pa anthu onseŵa ndine? Kodi ndidaŵabala ndine, kuti Inu muzindiwuza kuti ndiŵafungate pachifuwa panga, monga momwe mlezi amachitira poyamwitsa mwana, ndipo kuti ndipite nawo ku dziko limene mudalonjeza makolo ao molumbira kuti mudzaŵapatsa? Onani mutuwo |
Choncho woyangʼanira nyumba ya mfumu, bwanamkubwa wa mzinda, akuluakulu ena ndiponso olera anawo anatumiza uthenga uwu kwa Yehu: “Ife ndife atumiki anu ndipo tidzachita chilichonse chomwe mutiwuze. Sitidzasankha munthu wina aliyense kukhala mfumu ndipo chitani chimene mukuganiza kuti nʼchabwino kwa inu.”