Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 10:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Komanso pa nthawi yanu ya chisangalalo, pa maphwando anu oyikika ndi maphwando a mwezi watsopano, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu za chiyanjano, ndipo zidzakhala chikumbutso chanu pamaso pa Mulungu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu chikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu chikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pa tsiku lanu losangalala, pa masiku osankhidwa a zikondwerero zanu, ndi pa masiku oyamba a miyezi, mulize malipenga pamene mukupereka nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu zachiyanjano. Malipengawo adzakuthandizani kumkumbukira Mulungu wanu. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 10:10
34 Mawu Ofanana  

Mwamuna wakeyo anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukupita kwa iyeyo lero? Lero si tsiku la Chikondwerero cha Mwezi Watsopano kapena tsiku la Sabata.” Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”


Ansembe awa; Sebaniya, Yehosafati, Netaneli, Amasai, Zekariya, Benaya ndi Eliezara ndiwo ankayimba malipenga patsogolo pa Bokosi la Mulungu. Obedi-Edomu ndi Yehiya analinso alonda a pa khomo la bokosilo.


Kotero Aisraeli onse anabweretsa Bokosi la Chipangano la Yehova ndi mfuwu, ndiponso akuyimba zitoliro zanyanga zankhosa zazimuna, malipenga ndi maseche ndiponso akuyimba azeze ndi apangwe.


Hemani ndi Yedutuni anali oyangʼanira malipenga ndi ziwaya ndiponso zipangizo zina zoyimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni anawayika kuti aziyangʼanira pa chipata.


Kotero Alevi anayima okonzekera atanyamula zoyimbira za Davide ndiponso ansembe atanyamula malipenga awo.


Anthu onse anawerama pansi ndi kulambira, pamene oyimba amayimba ndi malipenga. Izi zonse zinapitirira mpaka pa mapeto pa nsembe zopsereza.


Ansembe anayimirira mʼmalo mwawo, monganso anachitira Alevi ndi zida zoyimbira za Yehova, zimene Davide anapanga zotamandira Yehova ndipo zimagwiritsidwa ntchito pamene amatamanda, ponena kuti, “Chikondi chake chikhale chikhalire.” Moyangʼanizana ndi Alevi, ansembe amaliza malipenga, ndipo Aisraeli onse anali atayimirira.


Amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Yehova, ansembe anabwera akuyimba malipenga, atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, anadza akuyimba matambolini ndi kutenga udindo wawo wotamanda Yehova, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraeli.


Ena mwa ana a ansembe amene ankayimba malipenga awo anali awa: Zekariya mwana wa Yonatani mwana wa Semaya mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu,


Mutamandeni poyimba malipenga, mutamandeni ndi pangwe ndi zeze.


Imbani lipenga la nyanga ya nkhosa yayimuna pa mwezi watsopano, ndi pamene mwezi waoneka wonse, pa tsiku la phwando;


ili ndi lamulo kwa Israeli, langizo la Mulungu wa Yakobo.


Ndi odala amene aphunzira kuyamika Inu, amene amayenda mʼkuwunika kwa nkhope yanu Yehova.


“Pamene Aaroni akulowa kumalo opatulika azivala chovala chapachifuwa cha zoweruzira chija chimene chalembedwa mayina a ana a Israeli kuti Yehova awakumbukire nthawi zonse.


Ulandire ndalama zopepeserazo kuchokera kwa Aisraeli ndipo zigwiritsidwe ntchito ya ku tenti ya msonkhano. Zoperekazi zidzakhala chikumbutso cha Aisraeli pamaso pa Yehova, ndiponso zowombolera miyoyo yanu.”


Ndipo tsiku limenelo lipenga lalikulu lidzalira. Amene akuzunzika ku Asiriya iwo amene ali ku ukapolo ku Igupto adzabwera ndi kudzalambira Yehova pa phiri lopatulika mu Yerusalemu.


“Uza Aisraeli kuti, ‘Tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, likhale tsiku lopumula, la msonkhano wopatulika, mulilengeze poyimba lipenga.


Pamene mukupita ku nkhondo mʼdziko lanu lomwe, kulimbana ndi mdani amene akukuzunzani, muziliza malipenga ochenjeza ndipo Yehova Mulungu wanu adzakukumbukirani ndi kukulanditsani mʼmanja mwa adani anu.


“Pa tsiku loyamba la mwezi uliwonse muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, onse wopanda chilema.


“ ‘Pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Ili ndi tsiku limene muziliza malipenga.


“Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.


Korneliyo anamuyangʼanitsitsa mngeloyo mwa mantha. Iye anafunsa kuti, “Nʼchiyani kodi Ambuye?” Mngelo anayankha kuti, “Mapemphero ako ndi zachifundo zako zafika pamaso pa Mulungu ngati chikumbutso.


Zidzachitika mwadzidzidzi, mʼkamphindi kochepa, monga ngati kuphethira kwa diso, pa lipenga lotsiriza. Pakuti lipenga lidzalira, akufa adzaukitsidwa opanda chovunda, ndipo ife tidzasandulika.


Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba.


Nʼchifukwa chake tsono muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.


Muzidzawawuza kuti, ‘Madzi a Yorodani analeka kuyenda pamene Bokosi la Chipangano la Yehova linkawoloka mtsinjewo. Miyala iyi idzakhala chikumbutso kwa anthu a Israeli kwa muyaya.’ ”


Ansembe asanu ndi awiri, atanyamula malipenga a nyanga za nkhosa zazimuna, akhale patsogolo pa Bokosi la Chipangano. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzazungulire mzindawu kasanu ndi kawiri ansembe akuliza malipenga.


Mzimu Woyera ndi mkwatibwi akuti, “Bwerani!” Ndipo amene akumva anena kuti Bwerani! Iye amene ali ndi ludzu abwere, ndipo aliyense amene afuna alandire mphatso yaulere ya madzi amoyo.


Ndipo Davide anati, “Taona mawa ndi tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano, ndipo ine ndiyenera kukadya ndi mfumu. Koma undilole ndipite ndikabisale mʼmunda mpaka mkuja madzulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa