Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 1:30 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Kuchokera mwa zidzukulu za Zebuloni: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

30 A ana a Zebuloni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 A ana a Zebuloni, kubadwa kwao, monga nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Mwa zidzukulu za Zebuloni adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 1:30
7 Mawu Ofanana  

Pamenepo Leya anati, “Mulungu wandipatsa mphatso yapamwamba. Tsopano mwamuna wanga adzandilemekeza chifukwa ndamubalira ana aamuna asanu ndi mmodzi.” Choncho anamutcha Zebuloni.


Ana aamuna a Zebuloni ndi awa: Seredi, Eloni ndi Yahaleeli.


“Zebuloni adzakhala mʼmphepete mwa nyanja; adzakhala pa dooko la sitima zapamadzi; malire ake adzafika ku Sidoni.


Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Isakara chinali 54,400.


Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa