Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 1:18 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, anasonkhanitsa anthu onse pamodzi. Anthuwo anafotokoza za makolo awo mwa mafuko awo ndi mabanja awo. Ndipo mayina a amuna onse amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo analembedwa, mmodzimmodzi

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

18 nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kutchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzimmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kutchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzimmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiŵiri, adasonkhanitsa mpingo wonse. Tsono Aisraele adalembetsa maina ao potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Ankalembetsa ndi anthu a zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo, mmodzimmodzi,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 1:18
7 Mawu Ofanana  

Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:


Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.


Atsogoleri a mafuko awo anali awa: Ana a Rubeni mwana wachisamba wa Israeli anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Awa anali mafuko a Rubeni.


Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai, mu tenti ya msonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, mʼchaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, kuti,


Mose ndi Aaroni anatenga anthu amene mayina awo anaperekedwa,


Alibe abambo kapena mayi, alibe chiyambi kapena chitsiriziro cha moyo wake. Iye ali ngati Mwana wa Mulungu ndipo akupitirira kukhala wansembe wamuyaya.


Melikizedeki sanali wochokera kwa Levi, komabe analandira chakhumi kuchokera kwa Abrahamu nadalitsa Abrahamuyo amene analandira malonjezo a Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa