Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 8:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!” Nthawi yomweyo anachiritsidwa khate lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Yesu adatambalitsa dzanja nkumukhudza, nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 8:3
19 Mawu Ofanana  

Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi.


Koma Naamani anachoka mokwiya ndipo anati, “Ine ndimaganiza kuti munthuyu atuluka ndipo ayimirira nayitana dzina la Yehova Mulungu wake, nayendetsa dzanja lake pamwamba pa nthendayi ndi kundichiritsa khate langa.


Choncho Naamani anapita ku Yorodani nakadzimiza mʼmadzimo kasanu nʼkawiri, monga momwe munthu wa Mulungu anamuwuzira. Thupi lake linakhalanso monga kale ndipo linakhala losalala ngati la kamnyamata.


Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo; Iye analamulira ndipo zinakhazikika.


Yehova anati, “Tsopano pisanso dzanja lako mʼmalaya.” Mose anapisanso dzanja lakelo mʼmalaya ake ndipo atalitulutsa, linali labwinobwino, ngati thupi lake lonse.


Pamenepo Yesu anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola ndipo linakhala monga linalili kale.


Yesu pomva naye chifundo, anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!”


Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, “Chete! Khala bata!” Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.


Anagwira dzanja lake nanena kwa iye, “Talita Kumi!” (Kutanthauza kuti, “Mtsikana, ndikunena ndi iwe, imirira!”)


Iye anayangʼana kumwamba ndipo ndi mawu otsitsa moyo, anati kwa iye, “Efataa!” (Kutanthauza kuti, “Tsekuka!”)


Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kumalowo, anadzudzula mzimu woyipawo kuti, “Iwe mzimu wolepheretsa kuyankhula ndi kumva, ndikulamulira tuluka mwa iye ndipo usadzalowenso.”


Ndipo kunali akhate ambiri ku Israeli mʼnthawi ya mneneri Elisa, koma panalibe mmodzi mwa iwo anachiritsidwa kupatula Naamani wa ku Siriya.”


Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo. Iye anati, “Ine ndikufuna, yeretsedwa!” Ndipo nthawi yomweyo khate lake linachoka.


Kenaka anapita nakakhudza chithatha cha maliro ndipo amene anachinyamulawo anayima. Iye anati, “Mnyamata, ndikukuwuza kuti, dzuka!”


Yesu atanena izi, Iye anayitana ndi mawu ofuwula kuti, “Lazaro, tuluka!”


Ine ndikanapanda kuchita pakati pawo zinthu zimene wina aliyense sanachitepo, iwo sakanakhala ochimwa. Koma tsopano aona zodabwitsa izi, komabe akundida Ine pamodzi ndi Atate anga.


Pakuti monga Atate amaukitsa akufa nawapatsa moyo, momwemonso Mwana amapereka moyo kwa amene Iye akufuna.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa