Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 5:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 “Odala ndi amene ali osauka mu mzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 “Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 5:3
55 Mawu Ofanana  

Ali pa mavuto akewo anafunafuna kuti Yehova Mulungu wake amukomere mtima ndipo anadzichepetsa kwakukulu pamaso pa Mulungu wa makolo ake.


Pemphero lake ndi momwe Mulungu anakhudzidwira ndi kupempha kwakeko, pamodzinso ndi machimo ake onse ndi kusakhulupirika kwake, ndiponso malo onse amene anamanga, malo azipembedzo ndi mafano a Asera ndi mafano asanadzichepetse, zonse zalembedwa mʼmbiri ya alosi.


Koma kusiyana ndi abambo ake Manase, iye sanadzichepetse pamaso pa Yehova. Amoni anawonjeza kulakwa kwake.


Pakuti mtima wako walapa, ndipo wadzichepetsa wekha pamaso pa Mulungu pamene unamva zimene Iye ananena motsutsa malo ano ndi anthu ake, ndipo chifukwa iwe unadzichepetsa wekha pamaso pa Ine ndi kungʼamba zovala zako ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, atero Yehova.


ngati anthu anga, amene amatchedwa ndi dzina langa adzichepetsa ndi kupemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zawo zoyipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwamba ndipo ndidzakhululuka tchimo lawo ndi kuchiritsa dziko lawo.


Nʼchifukwa chake ndi kuchita manyazi, ndikulapa podzithira fumbi ndi phulusa.”


Wodala munthu amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa, kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa, kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.


Tamandani Yehova. Wodala munthu amene amaopa Yehova, amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.


Odala ndi onse amene amaopa Yehova, amene amayenda mʼnjira zake.


Wodala ndi amene thandizo lake ndi Mulungu wa Yakobo.


Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye; kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu, pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa. Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.


Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.


Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.


Nsembe za Mulungu ndi mzimu wosweka; mtima wosweka ndi wachisoni Inu Mulungu simudzawunyoza.


Inu Yehova Wamphamvuzonse, wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.


Nʼkwabwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu oponderezedwa, kusiyana ndi kugawana zolanda ndi anthu onyada.


Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa, koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.


“Ndiye tsono ana inu, ndimvereni; odala anthu amene amasunga njira zanga.


Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima, iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo. Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!


Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.


Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine, chifukwa Yehova wandidzoza kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka. Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima, ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.


Kodi si manja anga amene anapanga zinthu zonsezi, motero zonsezi ndi zanga?” Akutero Yehova. “Koma munthu amene ndimakondwera naye ndi uyu: amene ali wodzichepetsa ndi wosweka mtima, ndipo amamvera mawu anga.


Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino. Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe? Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.


Pa nthawi imeneyo Yesu anati, “Ine ndikukuyamikani Inu Atate Ambuye akumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa Inu mwawabisira zinthu izi anzeru ndi ophunzira ndi kuziwulula kwa ana angʼonoangʼono.


Odala ndi munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”


Koma maso anu ndi odala chifukwa amapenya ndi makutu anu chifukwa amamva.


Yesu anati, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa.”


Chidzakhala chabwino kwa wantchitoyo ngati mbuye wake pofika adzamupeza akuchita zimenezi.


“Pamenepo mfumu idzati kwa a ku dzanja lamanja, ‘Bwerani inu odalitsika ndi Atate anga; landirani ufumu umene unakonzedwa chifukwa cha inu kuyambira pachiyambi cha dziko.


kuti, “Tembenukani mtima chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.”


Ndikuwuzani kuti ambiri adzabwera kuchokera kummawa ndi kumadzulo, nadzakhala nawo pa phwando pamodzi ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo mu ufumu wakumwamba.


Pamene Yesu anaona zimenezi anayipidwa. Anati kwa iwo, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse, pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa onga awa.


Koma Yesu anayankha kuti, “Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.”


“Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”


Ndipo Ine ndikupatsani inu ufumu, monga momwe Atate anga anandipatsiranso Ine,


kuti inu muthe kudya ndi kumwa pa tebulo langa mu ufumu wanga ndi kukhala pa mipando yaufumu kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli.”


“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine; chifukwa wandidzoza kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka. Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe ndi kwa osaona kuti apenyenso, kumasulidwa kwa osautsidwa,


Kenaka Yesu anamuwuza kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona Ine? Ndi odala amene amakhulupirira ngakhale asanaone.”


Kumbukirani mmene Yehova Mulungu wanu anakutsogolerani njira yonse mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kukutsitsani ndi kukuyesani kuti adziwe chimene chinali mu mtima mwanu ngati mungathe kusunga malamulo ake kapena ayi.


Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo.


Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.


Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda?


Kenaka mngelo anandiwuza kuti, “Lemba kuti, Odala amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anatinso, “Awa ndiwo mawu woona a Mulungu.”


“Odala amene achapa mikanjo yawo, kuti akhale ndi ufulu wopita ku mtengo wamoyo ndi kuti akalowe mʼzipata za mu mzindawo.


Iwe umati: ‘Ndine wolemera, ndine wachuma ndipo sindisowa kanthu.’ Koma sudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, waumphawi, wosaona ndi wamaliseche.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa