Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 26:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pamenepo akulu a ansembe ndi akuluakulu anasonkhana ku nyumba ya mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Nthaŵi imeneyo akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda adasonkhana m'nyumba ya mkulu wa ansembe onse, dzina lake Kayafa.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:3
23 Mawu Ofanana  

Iwo amakambirana, amandibisalira, amayangʼanitsitsa mayendedwe anga ndipo amakhala ndi chidwi chofuna kuchotsa moyo wanga.


Ndinali ngati mwana wankhosa wofatsa amene akupita naye kukamupha; sindinkadziwa kuti chiwembu chimene ankakonzekeracho chinkaloza ine. Iwo amati: “Tiyeni timuphe munthu ameneyu kuti dzina lake lisadzakumbukiridwenso.”


Koma ngati simundimvera; mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika ndi kumanyamula katundu nʼkumalowa naye pa zipata za Yerusalemu pa tsikuli, Ine ndidzabutsa moto pa zipata za Yerusalemu. Moto umenewo udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu ndipo moto wake sudzazima.’ ”


Tsopano Petro anakhala ku bwalo la nyumbayo, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye nati, “Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.”


Pamenepo asilikali abwanamkubwayo anamutenga nalowa naye ku bwalo la milandu ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali namuzungulira Iye.


Petro anamutsatira ali patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Kumeneko anakhala pansi ndi alonda namawotha moto.


Petro ali chakumunsi kwa bwalo la milandu, mmodzi wa atsikana a ntchito a mkulu wa ansembe anabwera.


Asilikali anamutenga Yesu ndi kupita naye mʼkati mwa nyumba yaufumu (dera lokhalako asilikali a mfumu) ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali.


Koma pamene anasonkha moto pakati pa bwalo la milandu, anakhala onse pansi ndipo Petro anakhalanso pansi.


Inalinso nthawi ya mkulu wa ansembe wa Anasi ndi Kayafa, pamene mawu a Mulungu anabwera kwa Yohane mwana wa Zakariya mʼchipululu.


Koma akulu a ansembe ndi Afarisi anapereka lamulo kuti ngati wina aliyense adziwe kumene kunali Yesu, iye akawawuze kuti akamugwire.


Kenaka Anasi anamutumiza Iye, ali womangidwabe, kwa Kayafa, mkulu wa ansembe.


Kenaka Ayuda anamutenga Yesu kuchoka kwa Kayafa ndi kupita ku nyumba yaufumu ya bwanamkubwa wa Chiroma. Tsopano kunali mmamawa, ndipo polewa kudetsedwa monga mwa mwambo Ayuda sanalowe mʼnyumba yaufumuyo; iwo anafuna kuti adye Paska.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa