Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 2:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 nafunsa kuti, “Ali kuti amene wabadwa kukhala mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kummawa ndipo tabwera kudzamupembedza.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Iwowo ankafunsa kuti, “Ali kuti mwana amene adabadwa kuti adzakhale Mfumu ya Ayuda? Ife tidaona nyenyezi yake ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 2:2
28 Mawu Ofanana  

“Ine ndakhazikitsa mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.”


Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako; mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.


Mitundu ya anthu idzatsata kuwunika kwako ndipo mafumu adzalondola kunyezimira kwa mʼbandakucha wako.


Yehova akuti, “Masiku akubwera, pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka. Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.


Mʼmalo mwake, adzatumikira Yehova Mulungu wawo ndiponso Davide mfumu yawo, amene ndidzawasankhira.


Sangalala kwambiri, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni! Fuwula, mwana wamkazi wa Yerusalemu! Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe, yolungama ndi yogonjetsa adani, yodzichepetsa ndi yokwera pa bulu, pa mwana wamphongo wa bulu.


“Ndikumuona iye koma osati tsopano; ndikumupenya iye koma osati pafupi. Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo; ndodo yaufumu idzatuluka mwa Israeli. Iye adzagonjetsa Mowabu ndi kugonjetsa ana onse a Seti.


Mfumu Herode atamva zimenezi, anavutika mu mtima kwambiri pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu.


“Uza mwana wamkazi wa Ziyoni, taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe, yofatsa ndi yokwera pa bulu, pa kamwana ka bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.”


Pa nthawi yomweyo Yesu anayimirira pamaso pa bwanamkubwa ndipo bwanamkubwayo anamufunsa Iye kuti, “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Koma Yesu anayankha kuti, “Mwanena ndinu.”


“Yodala mfumu imene ikubwera mʼdzina la Ambuye!” “Mtendere kumwamba ndi ulemerero mmwambamwamba!”


Lero mʼmudzi wa Davide wakubwadwirani Mpulumutsi; Iye ndi Khristu Ambuye.


Pamenepo Pilato anamufunsa Yesu kuti, “Kodi Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.”


Ndipo panalembedwa chikwangwani pamwamba pake chimene chinati: uyu ndi mfumu ya ayuda.


Kenaka Natanieli ananena kuti, “Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu; Inu ndinu Mfumu ya Israeli.”


Iwo anatenga nthambi za kanjedza ndi kupita kukakumana naye, akufuwula kuti, “Hosana! “Wodala Iye amene akubwera mʼdzina la Ambuye! “Yodala Mfumu ya Israeli!”


Pilato anati, “Kani ndiwe mfumu!” Yesu anayankha kuti, “Inu mwalondola ponena kuti, Ine ndine mfumu. Kunena zoona, Ine ndinabadwa chifukwa cha chimenechi, ndipo nʼchifukwa chake ndinabwera mʼdziko lapansi, kudzachitira umboni choonadi. Aliyense amene ali mbali yachoonadi amamvera mawu anga.”


Pilato analemba chikwangwani chomwe anachikhoma pa mtandapo. Panalembedwa mawu akuti, yesu wa ku nazareti, mfumu ya ayuda.


Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye wanga ndi Mulungu wanga!”


kuti aliyense alemekeze Mwanayo monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana salemekezanso Atate amene anamutuma Mwanayo.


Pamenepo munthuyo anati, “Ambuye, ndikukhulupirira,” ndipo anamulambira Iye.


Pamene Mulungu amatuma Mwana wake woyamba kubadwa ku dziko lapansi anati, “Angelo onse a Mulungu amupembedze Iye.”


“Ine Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti achitire umboni uwu ku mipingo. Ine ndine Muzu ndi Chipatso cha Davide ndipo ndine Nthanda Yonyezimira.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa