Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 1:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Buku lofotokoza za mʼbado wa Yesu Khristu mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu:

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Yesu Khristu, makolo ake anali Davide ndi Abrahamu. Motsatanatsatana maina a makolo ake onse ndi aŵa:

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 1:1
39 Mawu Ofanana  

Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe, ndi kutemberera amene adzatemberera iwe; ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa iwe.”


Mbiri ya momwe kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera pa tsiku lija Yehova Mulungu ankazilenga ndi iyi: Yehova Mulungu atapanga dziko lapansi ndi kumwamba,


ndipo kudzera mwa chidzukulu chako, mitundu yonse ya anthu pa dziko lapansi idzadalitsika, chifukwa iwe wandimvera.”


Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu.


Yehova analumbira kwa Davide, lumbiro lotsimikizika kuti Iye sadzasintha: “Mmodzi wa ana ako ndidzamuyika pa mpando waufumu;


Inu munati, “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga, ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,


kuti zidzukulu zake zidzakhale kwamuyaya ndipo mpando wake waufumu udzakhazikika pamaso panga ngati dzuwa;


Padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese ndipo nthambi idzaphukira kuchokera ku mizu yake.


Atatha kumugwira mwankhanza ndikumuyimba mlandu, kenaka anapita naye kukamupha. Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake, poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo? Ndani anaganizirapo poona kuti iye anakanthidwa chifukwa cha zolakwa za anthu anga?


Yehova akuti, “Masiku akubwera, pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka. Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.


monga ndachita zimenezi motsimikiza, choncho ndidzasunga pangano limene ndinachita ndi zidzukulu za Yakobo ndi Davide mtumiki wanga. Ndidzasankha mmodzi mwa ana a Davide kuti alamulire zidzukulu za Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Komatu ndidzawamvera chifundo ndi kuwakhazikanso pabwino.’ ”


“Tsiku limenelo ndidzabwezeretsa nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzakonzanso malo amene anagumuka, ndi kuyimanganso monga inalili poyamba,


Pa tsiku limenelo Yehova adzatchinjiriza onse okhala mu Yerusalemu, kotero kuti anthu ofowoka kwambiri pakati pawo adzakhala ngati Davide, ndipo nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mngelo wa Yehova wowatsogolera.


Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera.


Abrahamu anabereka Isake, Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka Yuda ndi abale ake.


Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, “Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda.”


Yesu atangobatizidwa, nthawi yomweyo potuluka mʼmadzi, kumwamba kunatsekuka ndipo taonani, Mzimu wa Mulungu anatsika ngati nkhunda natera pa Iye.


Yesu atapitirira ulendo wake, amuna awiri osaona anamutsatira Iye, akufuwula kuti, “Tichitireni chifundo, Mwana wa Davide!”


ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha.”


Kodi Malemba samanena kuti Khristu adzachokera mʼbanja la Davide, ndi ku Betelehemu mu mzinda umene Davide anakhalamo?”


Koma iye anali mneneri ndipo anadziwa kuti Mulungu analonjeza ndi lumbiro kuti adzayika mmodzi wa zidzukulu zake pa mpando waufumu.


Uthengawu ndi wonena za Mwana wake amene mwa umunthu wake anali wochokera mwa Davide.


Abrahamu ndi zidzukulu zake sanalandire lonjezano lakuti adzalandira dziko lapansi kudzera mu Malamulo, koma kudzera mu chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.


Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni.


Malonjezo awa anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Malemba sakunena kuti, “kwa mbewu zake,” kutanthauza anthu ambiri, koma, “kwa mbewu yako,” kutanthauza munthu mmodzi, amene ndi Khristu.


Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu.


Kumbukira Yesu Khristu wochokera ku mtundu wa Davide kuti anauka kwa akufa. Uwu ndiye uthenga wanga wabwino


“Ine Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti achitire umboni uwu ku mipingo. Ine ndine Muzu ndi Chipatso cha Davide ndipo ndine Nthanda Yonyezimira.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa