Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 99:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova; Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Yehova ndiye wamkulu mu Ziyoni; ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Yehova ndiye wamkulu m'Ziyoni; ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Chauta ndi wamkulu ku Ziyoni. Ali pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 99:2
15 Mawu Ofanana  

Yehova wakwezeka pa anthu a mitundu yonse, ulemerero wake ndi woposa mayiko akumwamba.


Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu; anayika anthu pansi pa mapazi athu.


Mulungu akulamulira mitundu ya anthu; Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.


Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiri Mulungu akuwala.


Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina. Anthu owukira asadzitukumule.


Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi; ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.


Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni; pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”


Kodi tidzawayankha chiyani amithenga a ku Filisitiya? “Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo mu mzinda wakewu, anthu ozunzika apeza populumukira.”


“Palibe kuwukira kulikonse kumene wakuona mwa Yakobo, sanaone chovuta mu Israeli. Yehova Mulungu wawo ali nawo: mfuwu wa mfumu uli pakati pawo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa