Masalimo 101:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa pamaso panga. Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro; iwo sadzadziphatika kwa ine. Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chachabechabe. Ndimadana ndi zochita za anthu okusiyani, sizindikomera konse. Onani mutuwo |
Musayesere ndi pangʼono pomwe kusunga maganizo oyipa awa mu mtima mwanu: “Chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka chokhululukirana ngongole, chayandikira,” kuti musaonetse mtima woyipa kwa mʼbale wanu wosauka nʼkusamupatsa chilichonse. Iye angadzakunenereni inu mlandu kwa Ambuye, ndipo mudzapezeka wochimwa.