Masalimo 1:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake ndipo masamba ake safota. Chilichonse chimene amachita amapindula nacho. Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino. Onani mutuwo |
Mʼmbali zonse za mtsinje mudzamera mitengo ya zipatso zakudya za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota kapena kulephera kubereka zipatso. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake adzakhala ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya ndipo masamba ake azidzachitira mankhwala.”