Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 5:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye analenga mwamuna ndi mkazi. Anawadalitsa ndipo anawatcha “Munthu.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nawadalitsa iwo natcha mtundu wao anthu, tsiku lomwe anawalenga iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nawadalitsa iwo natcha mtundu wao anthu, tsiku lomwe anawalenga iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Adalenga mwamuna ndi mkazi, ndipo adaŵadalitsa, naŵatchula dzina loti Anthu.)

Onani mutuwo Koperani




Genesis 5:2
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.


Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.”


Yehova Mulungu anatenga munthu uja ndi kumuyika mʼmunda wa Edeni kuti awulime ndi kuwusamalira.


Munthu uja anati, “Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga; adzatchedwa ‘mkazi,’ popeza wachokera mwa mwamuna.”


Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti.


Kodi Yehova sanawalenge iwo ngati munthu mmodzi? Ndi ake mʼthupi ndi mu mzimu. Nʼchifukwa chiyani ali mmodzi? Chifukwa Iye amafuna ana opembedza Mulungu. Motero samala moyo wako wauzimu, ndipo usakhale wosakhulupirika kwa mkazi wa unyamata wako.


Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge kuti pachiyambi Mulungu analenga iwo, ‘mwamuna ndi mkazi?’


Koma pachiyambi cha chilengedwe, Mulungu ‘analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.’


Kuchoka kwa munthu mmodzi Iye analenga mtundu uliwonse wa anthu, kuti akakhale pa dziko lonse lapansi; ndipo Iye anakonzeratu nthawi yawo ndiponso malo enieni kumene adzakhale.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa