Genesis 4:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?” Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?” Onani mutuwoBuku Lopatulika9 Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang'anira mphwanga? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang'anira mphwanga? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Tsono Chauta adafunsa Kainiyo kuti, “Kodi mng'ono wako Abele ali kuti?” Iye adayankha kuti, “Sindikudziŵa. Kodi ndi ntchito yanga kusamala mng'ono wangayo?” Onani mutuwo |
Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza.