Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 4:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, “Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Adamu adakhala ndi mkazi wake Heva ndipo mkaziyo adatenga pathupi. Tsono adabala mwana wamwamuna, ndipo adati, “Ndalandira mwana wamwamuna mwa chithandizo cha Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Kaini.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 4:1
8 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzayika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; Iye adzaphwanya mutu wako ndipo iwe udzaluma chidendene chake.”


Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo.


Kenaka anabereka mʼbale wake Abele. Abele anali woweta nkhosa ndipo Kaini anali mlimi.


Adamu anagonanso malo amodzi ndi mkazi wake, ndipo anabereka mwana wamwamuna namutcha Seti, kutanthauza kuti, “Mulungu wandipatsa mwana wina mʼmalo mwa Abele, popeza Kaini anamupha.”


Ndipo anamutcha Nowa ndipo anati, “Iyeyu adzatipumulitsa ku ntchito zathu zolemetsazi, zolima nthaka imene Yehova anayitemberera.”


Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova, ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.


Tsopano iphani munthu wamwamuna aliyense. Ndiponso iphani mayi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna,


Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa