Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 3:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Kenaka maso awo anatsekuka, ndipo anazindikira kuti anali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nadzipangira zovala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amaliseche: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira matewera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amaliseche: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira matewera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Atangodya choncho, adazindikira kuti ali maliseche. Choncho adasoka masamba a mkuyu navala.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 3:7
13 Mawu Ofanana  

Munthu uja ndi mkazi wakeyo, onse awiri anali maliseche ndipo analibe manyazi.


“Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye zipatso za mu mtengowo, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wodziwa zabwino ndi zoyipa.”


Atalowa mu mzinda wa Samariya, Elisa anati, “Yehova tsekulani maso a anthu awa kuti aone.” Choncho Yehova anatsekula maso awo ndipo anangoona kuti ali mʼkati mwenimweni mwa Samariya.


Mudzakhala ngati munthu wogona pa bedi lalifupi kwambiri kuti sangathe kutambalitsapo miyendo; ndiponso mudzakhala ngati munthu amene wafunda bulangeti lochepa kwambiri kuti sangathe nʼkufunda komwe.


Maliseche ako adzakhala poyera ndipo udzachita manyazi. Ndidzabwezera chilango ndipo palibe amene adzandiletse.”


Ukonde wawo wa kangawude sangawuvale ngati chovala; ndipo chimene apangacho sangachifunde. Ntchito zawo ndi zoyipa, ndipo amakonda kuchita zandewu ndi manja awo.


Yerusalemu wachimwa kwambiri ndipo potero wakhala wodetsedwa. Onse amene ankamulemekeza pano akumunyoza, chifukwa aona umaliseche wake. Iye mwini akubuwula ndipo akubisa nkhope yake.


Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake.


ndipo ziwalo zathupi zimene timaziyesa zopanda ulemu, ndizo timazilemekeza kwambiri. Ndipo ziwalo zosaoneka bwino ndizo zimalandira ulemu wapadera.


Zimene muzidzaziona zidzakusokonezani mitu.


(Yehova anachita izi kuti Aisraeli onse aphunzire kumenya nkhondo; makamaka amene nʼkale lonse sanadziwe kumenya nkhondo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa