Genesis 3:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 “Ndithudi simudzafa,” inatero njokayo kwa mkaziyo. Onani mutuwoBuku Lopatulika4 Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Koma njokayo idayankha mkaziyo kuti, “Iyai, kufa simudzafa konse. Onani mutuwo |
Iwo anayankha kuti, “Munthu wina anabwera kudzakumana nafe, ndipo anatiwuza kuti, bwererani kwa mfumu imene inakutumani ndipo mukayiwuze kuti, ‘Yehova akuti, kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni? Tsono sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’ ”
Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza.