Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 26:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Choncho Abimeleki anamuyitanitsa Isake nati, “Uyu ndi mkazi wako ndithu! Nanga bwanji umati, ‘Ndi mlongo wanga’?” Ndipo Isake anamuyankha kuti, “Ine ndimaganiza kuti ndingataye moyo wanga chifukwa cha iyeyu.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Ndipo Abimeleki anamuitana Isaki nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isaki anati kwa iye, Chifukwa ndinati, Ndingafe chifukwa cha iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Abimeleki anamuitana Isaki nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isaki anati kwa iye, Chifukwa ndinati, Ndingafe chifukwa cha iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Apo Abimeleki adatuma munthu kukaitana Isaki. Ndipo adati, “Ameneyu ndi mkazi wako ndithu. Bwanji mujamu unkanena kuti ndi mlongo wako?” Iye adayankha kuti, “Ndinkaganiza kuti ndidzaphedwa ndikanena kuti ndi mkazi wanga.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 26:9
5 Mawu Ofanana  

Choncho Farao anayitanitsa Abramu namufunsa kuti, “Nʼchiyani wandichitirachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiwuze kuti ameneyu ndi mkazi wako?


Tsono Abimeleki anati, “Nʼchiyani chimene watichitira? Mmodzi mwa anthuwa anatsala pangʼono kugona ndi mkazi wako ndipo ukanatisandutsa ife kukhala olakwa.”


Isake atakhalako kumeneko nthawi yayitali, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anasuzumira pa zenera kuyangʼana kunja, ndipo anaona Isake akugwiragwira Rebeka, mkazi wake.


Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe Filipo, ndakhala pakati panu nthawi yonseyi ndipo iwe sukundidziwabe? Aliyense amene waona Ine, waonanso Atate. Tsono ukunena bwanji kuti, ‘Tionetseni Atate?’


Pamenepo Petro anazindikira nati, “Tsopano ndikudziwa mosakayika kuti Ambuye anatuma mngelo wake kudzandipulumutsa mʼmanja mwa Herode, ndi ku zoyipa zonse zimene Ayuda amafuna kundichitira.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa