Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 26:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Zidzukulu zako ndidzazichulukitsa ngati nyenyezi za mu mlengalenga ndi kuzipatsa mayiko onsewa. Ndiponso anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 ndipo ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 ndipo ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka monga momwe ziliri nyenyezi zakuthambo, ndipo zidzukulu zakozo ndidzazipatsa maiko onseŵa. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa zidzukulu zako.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 26:4
22 Mawu Ofanana  

Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati fumbi lapansi moti amene angathe kuwerenga fumbilo ndiye kuti angathenso kuwerenga zidzukulu zako.


Pa tsiku limenelo, Yehova anachita pangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako, kuchokera ku mtsinje wa ku Igupto mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.


Yehova anapita naye Abramu panja nati, “Tayangʼana kumwambaku, ndipo chifukwa cha chimenechi uwerenge nyenyezi ngati ungathe kuziwerenga.” Ndipo anamuwuza kuti, “Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.”


Abrahamu adzakhaladi mtundu wa anthu waukulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya anthu pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa iye.


Usiku umenewo Yehova anadza kwa Isake nati, “Ine ndine Mulungu wa abambo ako Abrahamu. Usachite mantha popeza Ine ndili ndi iwe. Ndidzakudalitsa ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri chifukwa cha mtumiki wanga Abrahamu.”


Zidzukulu zako zidzachuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi ndipo zidzabalalikira kumadzulo ndi kummawa, kumpoto ndi kummwera. Anthu onse adzalandira madalitso kudzera mwa iwe ndi zidzukulu zako.


Mulungu Wamphamvuzonse akudalitse iwe nakupatse ana ambiri mpaka udzasanduke gulu lalikulu la mitundu ya anthu.


Dziko limene ndinapereka kwa Abrahamu ndi Isake ndiliperekanso kwa iwe. Lidzakhala lako ndi la zidzukulu zako.”


Tsono Aisraeli anakhazikika mʼdziko la Igupto ku chigawo cha Goseni. Kumeneko anapeza chuma ndipo anaberekana nachuluka kwambiri.


Davide sanawerenge amuna amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kucheperapo, chifukwa Yehova analonjeza kuti adzachulukitsa Aisraeli ngati nyenyezi zamumlengalenga.


Dzina lake likhazikike kwamuyaya, lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa. Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye ndipo iwo adzamutcha iye wodala.


Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isake, Israeli ndi zija munawalonjeza polumbira pa dzina lanu kuti, ‘Ine ndidzachulukitsa zidzukulu zanu ndipo zidzakhala zambiri ngati nyenyezi zakumwamba. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonseli limene ndinalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lawo nthawi zonse.’ ”


Ndinakhazikitsa pangano langa ndi iwo kuwalonjeza kuti ndidzawapatsa dziko la Kanaani kumene anakhalako kale ngati alendo.


Inu ndinu ana a aneneri ndiponso ana apangano limene Mulungu anachita ndi makolo anu. Iye anati kwa Abrahamu, ‘Anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako.’


Malonjezo awa anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Malemba sakunena kuti, “kwa mbewu zake,” kutanthauza anthu ambiri, koma, “kwa mbewu yako,” kutanthauza munthu mmodzi, amene ndi Khristu.


Malemba anaonetseratu kuti Mulungu adzalungamitsa anthu a mitundu ina mwachikhulupiriro, ndipo ananeneratu Uthenga Wabwino kwa Abrahamu kuti, “Mitundu yonse ya anthu idzadalitsika kudzera mwa iwe.”


Musapezeke ndi kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa kuti Yehova abweze mkwiyo wake wochititsa manthawu. Adzakuchitirani chifundo ndi kukumverani chisoni, ndipo adzakuchulukitsani monga analonjeza mwa lumbiro kwa makolo anu,


Sukalowa ndi kutenga dziko lawolo chifukwa cha kulungama kwako kapena kukhulupirika kwako koma chifukwa cha kuyipa kwa anthuwo. Yehova Mulungu wako awapirikitsa pamaso pako kuti akwaniritse zimene analumbira kwa makolo ako Abrahamu, Isake ndi Yakobo.


Ndi chikhulupiriro chimenechi makolo athu akale anayamikidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa