Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 26:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Khala mʼdziko lino ndipo ndidzakhala nawe ndi kukudalitsa. Pakuti kwa iwe ndi zidzukulu zako ndidzapereka mayiko onsewa. Choncho ndidzakwaniritsa pangano limene ndinalumbira kwa Abrahamu, abambo ako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Khala kuno ndipo Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakudalitsa chifukwa ndidzapereka maiko onseŵa kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako. Ndidzasunga lumbiro limene ndidachita kwa bambo wako Abrahamu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 26:3
42 Mawu Ofanana  

Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe.


Dziko lonse ukulionalo ndidzalipereka kwa iwe ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.


Dzuka ndipo uyendere dziko lonseli mulitali ndi mulifupi pakuti ndalipereka kwa iwe.”


Pa tsiku limenelo, Yehova anachita pangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako, kuchokera ku mtsinje wa ku Igupto mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.


Koma Mulungu anati, “Ayi, koma mkazi wako Sara adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha Isake. Ndidzasunga pangano langa losatha ndi iyeyu komanso ndi zidzukulu zobwera pambuyo pake.


Dziko lonse la Kanaani, limene iwe ukukhala tsopano, ndalipereka kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako kuti likhale chuma chanu mpaka muyaya. Ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wa zidzukulu zako.”


Abrahamu anachokako kumeneko napita ku Negevi ndipo anakakhala ku dziko la Gerari, limene lili pakati pa mzinda wa Kadesi ndi mzinda wa Suri. Anakhala ku Gerari kwa kanthawi,


Atamwalira Abrahamu, Mulungu anadalitsa mwana wake Isake, amene ankakhala pafupi ndi Beeri-lahai-roi (chitsime cha Wamoyo Wondipenya).


Isake anadzala mbewu mʼmunda, ndipo chaka chomwecho anakolola zinthu zambiri chifukwa Yehova anamudalitsa.


Anali ndi nkhosa, ngʼombe ndi antchito ambiri mwakuti Afilisti anamuchitira nsanje.


Usiku umenewo Yehova anadza kwa Isake nati, “Ine ndine Mulungu wa abambo ako Abrahamu. Usachite mantha popeza Ine ndili ndi iwe. Ndidzakudalitsa ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri chifukwa cha mtumiki wanga Abrahamu.”


Tsono Yehova anayimirira pambali pake, nati, “Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu kholo lake la Isake abambo ako. Ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako dziko limene ukugonamolo.


Ine ndili nawe pamodzi ndipo ndidzakuyangʼanira kulikonse upiteko, ndipo ndidzakubwezera ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zimene ndakulonjezazi.”


Pamenepo Yehova anati kwa Yakobo, “Bwerera ku dziko la makolo ako ndi kwa abale ako, ndipo Ine ndidzakhala nawe.”


Dziko limene ndinapereka kwa Abrahamu ndi Isake ndiliperekanso kwa iwe. Lidzakhala lako ndi la zidzukulu zako.”


Koma Yehova anali ndi Yosefe ndipo zake zonse zimayenda bwino. Iye ankakhala mʼnyumba ya mbuye wake wa ku Igupto.


koma Yehova anali naye, ndipo anamuonetsa kukoma mtima kwake, kotero kuti woyangʼanira ndende anakondwera ndi Yosefe.


Kenaka Israeli anati kwa Yosefe, “Ine ndatsala pangʼono kufa, koma Mulungu adzakhala ndipo adzakutenganinso kubwerera nanu ku dziko la makolo anu.


Kenaka Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndatsala pangʼono kufa. Koma mosakayika Mulungu adzakuyangʼanirani nadzakutengani kukutulutsani mʼdziko lino kupita ku dziko limene Iye analonjeza kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.”


pangano limene anachita ndi Abrahamu, lonjezo limene analumbira kwa Isake.


Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya, mawu amene analamula kwa mibado yonse,


pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu, lumbiro limene analumbira kwa Isake.


Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo; ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.


“Imvani pemphero langa Inu Yehova, mverani kulira kwanga kopempha thandizo; musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu, popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa; monga anachitira makolo anga onse.


Mulungu anamva kubuwula kwawo ndipo anakumbukira pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo.


Ndipo Mulungu anati, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe kuti ndine amene ndakutuma; Ukadzatulutsa anthu anga mʼdziko la Igupto, udzapembedza Mulungu pa phiri lino.”


Ndinakhazikitsa pangano langa ndi iwo kuwalonjeza kuti ndidzawapatsa dziko la Kanaani kumene anakhalako kale ngati alendo.


Ndidzakutengani kukhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼgoli la Aigupto.


Ndipo ndidzakufikitsani ku dziko limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo. Ndidzakupatsani dziko limenelo kuti likhale lanu. Ine ndine Yehova.’ ”


Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe; ndipo pamene ukuwoloka mitsinje, sidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto, sudzapsa; lawi la moto silidzakutentha.


Usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe; ndidzabweretsa ana ako kuchokera kummawa, ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kumadzulo.


Mudzakhala wokhulupirika kwa Yakobo, ndi kuonetsa chifundo chanu kwa Abrahamu, monga munalonjeza molumbira kwa makolo athu masiku amakedzana.


Mulungu si munthu kuti aname, kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake. Kodi amayankhula koma osachita? Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa?


Taonani, Ine ndakupatsani dziko ili. Lowani ndi kulilanda dziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo komanso kwa zidzukulu zawo.”


Kenaka Yehova anawuza Mose kuti, “Limenelo ndi dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo pamene ndinanena kuti, ‘Ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’ Ndakulola kuti ulione, koma sudzawoloka kuti ukalowemo.”


Muzichita chilichonse chimene mwaphunzira kapena kulandira kapena kumva kuchokera kwa ine kapena mwaona mwa ine. Ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.


Ndi chikhulupiriro chomwecho anakhala ngati mlendo mʼdziko lija limene Mulungu anamulonjeza. Anakhala mʼmatenti monganso anachitira Isake ndi Yakobo, amene nawonso analonjezedwanso.


Momwemonso Mulungu pofuna kutsimikizira anthu amene adzalandire lonjezo, kuti Iye sangasinthe maganizo, anatsimikiza lonjezo lakelo ndi lumbiro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa