Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 26:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yehova anadza kwa Isake nati, “Usapite ku Igupto; koma ukhale mʼdziko limene ndidzakuwuza kuti ukakhalemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Ndipo Yehova anamuonekera iye nati, Usatsikire ku Ejipito, khala m'dziko m'mene ndidzakuuza iwe;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Yehova anamuonekera iye nati, Usatsikire ku Ejipito, khala m'dziko m'mene ndidzakuuza iwe;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono Chauta adaonekera Isaki namuuza kuti, “Usapite ku Ejipito, koma ukhale m'dziko limene ndidzakuuza kuti ukhalemo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 26:2
11 Mawu Ofanana  

Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, “Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.


Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe.


Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse.


Koma Mulungu anati, “Ayi, koma mkazi wako Sara adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha Isake. Ndidzasunga pangano langa losatha ndi iyeyu komanso ndi zidzukulu zobwera pambuyo pake.


Yehova anadza kwa Abrahamu pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya thundu ya ku Mamre. Abrahamu nʼkuti atakhala pansi pa khoma la tenti yake masana, dzuwa likutentha.


Usiku umenewo Yehova anadza kwa Isake nati, “Ine ndine Mulungu wa abambo ako Abrahamu. Usachite mantha popeza Ine ndili ndi iwe. Ndidzakudalitsa ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri chifukwa cha mtumiki wanga Abrahamu.”


Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova? Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate.


Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino; khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika.


Mulungu anamva kubuwula kwawo ndipo anakumbukira pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo.


Ine ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo, pangano langa ndi Isake, pangano langa ndi Abrahamu. Ndidzakumbukiranso dzikolo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa