Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 2:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Tsono Yehova Mulungu anawumba munthu kuchokera ku dothi nawuziramo mpweya wamoyo mʼmphuno mwake ndipo munthuyo anakhala wamoyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono Chauta adatenga dothi pa nthaka, ndipo adaumba munthu ndi dothilo. Adamuuzira mpweya wopatsa moyo m'mphuno zake, ndipo munthuyo adakhala wamoyo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 2:7
33 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.


koma kasupe ankatuluka mʼnthaka ndi kuthirira pa dziko lonse.


Kuti upeze chakudya udzayenera kukhetsa thukuta, mpaka utabwerera ku nthaka pakuti unachokera kumeneko; pakuti ndiwe fumbi ku fumbi komweko udzabwerera.”


Kotero Yehova Mulungu anatulutsa Adamu Mʼmunda wa Edeni kuti azilima mʼnthaka imene anachokera.


Chilichonse chamoyo, chokhala pa mtunda chinafa.


nthawi zonse pamene ndili ndi moyo, mpweya wa Mulungu uli mʼmphuno mwanga,


Mzimu wa Mulungu wandiwumba, mpweya wa Wamphamvuzonse umandipatsa moyo.


Ine ndili monga inu pamaso pa Mulungu; nanenso ndinachokera ku dothi.


nanga kuli bwanji ndi iwo amene amakhala mʼnyumba zadothi, amene maziko awo ndi fumbi, amene amathudzuka mosavuta ngati kadziwotche!


Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.


pakuti Iye amadziwa momwe tinawumbidwira, amakumbukira kuti ndife fumbi.


Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Yehova; imafufuza ziwalo zake zonse zamʼkati.


Iyi ndi nthawi imene thupi lidzabwerera ku dothi, kumene linachokera, mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene anawupereka.


Nthawi yongʼamba ndi nthawi yosoka, nthawi yokhala chete ndi nthawi yoyankhula.


Lekani kudalira munthu, amene moyo wake sukhalira kutha. Iye angathandize bwanji wina aliyense?


Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu. Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba; ife tonse ndi ntchito ya manja anu.


Wodzozedwa wa Yehova, mpweya wathu wotipatsa moyo, anakodwa mʼmisampha yawo. Tinaganiza kuti tidzakhala pansi pa mthunzi wake pakati pa mitundu ya anthu.


Uwawuze kuti zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kwa mafupa ndi izi: Ndidzawuzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo.


Ndidzakupatsani mitsempha ndi mnofu. Ndiponso ndidzakukutani ndi khungu. Pambuyo pake ndidzawuzira mpweya mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”


Uthenga wa Yehova kwa Israeli. Yehova, amene amayala mlengalenga, amene amayika maziko a dziko lapansi, ndiponso amene amalenga mzimu wokhala mwa munthu, akunena kuti,


Koma Mose ndi Aaroni anadzigwetsa chafufumimba ndipo analira mokweza, “Chonde Mulungu, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, kodi mudzakwiyira gulu lonse pamene munthu mmodzi yekha ndiye amene wachimwa?”


“Ngati nʼkotheka Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, sankhani munthu woti ayangʼanire gulu ili kuti


Ndi mawu amenewo Iye anawapumira ndipo anati, “Landirani Mzimu Woyera.


Ndipo satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti Iye amasowa kanthu, chifukwa Iye ndiye amapereka moyo ndi mpweya kwa anthu onse ndi zina zonse.


Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? “Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’ ”


Kwalembedwa kuti, “Munthu woyamba Adamu anakhala wamoyo,” Adamu wotsiriza anakhala wopatsa moyo.


Munthu woyamba anali wa dziko lapansi, wochokera mʼnthaka koma munthu wachiwiri anali wochokera kumwamba.


Koma tili ndi chuma ichi mʼmbiya zadothi, kusonyeza kuti mphamvu yoposayi, imachokera kwa Mulungu osati kwa ife.


Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu.


Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa kenaka Hava.


Komanso, tonsefe tinali ndi abambo athu otibala amene amatilanga ndipo timawapatsa ulemu. Nanga kodi sitidzagonjera Atate a mizimu yathu kuti tikhale ndi moyo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa