Genesis 2:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Pofika tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito zonse zimene ankagwira ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anapumula ku ntchito zake zonse. Onani mutuwoBuku Lopatulika2 Tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri ku ntchito yake yonse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri ku ntchito yake yonse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi Mulungu adamaliza ntchito imene ankachitayo, ndipo adapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Onani mutuwo |
koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi kapena wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu kapena ngʼombe yanu kapena bulu wanu kapena ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu, motero ndiye kuti wantchito wanu wamwamuna ndi wantchito wanu wamkazi adzapumula monga inuyo.