Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 2:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Motero kumwamba, dziko lapansi ndi zonse za mʼmenemo zinatha kulengedwa monga mwa kuchuluka kwawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lao lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lao lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Motero dziko lonse lapansi, thambo ndi zonse zokhala m'menemo, zidatha kulengedwa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 2:1
34 Mawu Ofanana  

Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.


Mbiri ya momwe kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera pa tsiku lija Yehova Mulungu ankazilenga ndi iyi: Yehova Mulungu atapanga dziko lapansi ndi kumwamba,


Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, Inu amene mumakhala pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Ndipo Hiramu anawonjezera kunena kuti, “Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi! Iye wamupatsa Davide mwana wanzeru, wodzaza ndi luntha ndi wozindikira, amene adzamanga Nyumba ya Mulungu ndi kudzimangira yekha nyumba yaufumu.


Inu nokha ndiye Yehova. Munalenga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, zolengedwa zonse zimene zili mʼmenemo. Munalenga dziko ndi zonse zokhalamo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo. Zonse mumazisunga ndi moyo ndipo zonse za kumwamba zimakupembedzani.


Kodi mwa zonsezi ndi chiti chimene sichidziwa kuti lachita zimenezi ndi dzanja la Yehova?


Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala; watambasula miyamba ngati tenti


Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo; Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.


Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa, zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.


Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo; Iye analamulira ndipo zinakhazikika.


Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera.


Tsiku la Sabata lidzakhala chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi Aisraeli chosonyeza kuti Yehova analenga za kumwamba ndi dziko lapansi kwa masiku asanu ndi limodzi ndi kuti pa tsiku lachisanu ndi chiwiri analeka kugwira ntchito napumula.”


Dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zidzasungunuka ndipo mlengalenga mudzakulungidwa ngati chipepala; nyenyezi zonse zidzayoyoka ngati masamba ofota a mphesa, ngati masamba onyala a mtengo wa mkuyu.


Yehova Mulungu amene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika, amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka, amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo, ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti,


Ndine amene ndinapanga dziko lapansi ndikulenga munthu kuti akhalemo. Ine ndi manja anga ndinayalika thambo; ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga.


Yehova analenga zinthu zakumwamba, Iye ndiye Mulungu; amene akulenga dziko lapansi, ndi kulikhazikitsa, sanalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma analipanga kuti anthu akhalemo. Iyeyu akunena kuti: Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.


Inde dzanja langa linamanga maziko a dziko lapansi, dzanja langa lamanja linafunyulula mlengalenga. Ndi mawu anga ndinalenga kumwamba ndi dziko lapansi.


“Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.


“Taonani, ndikulenga mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukika, zidzayiwalika kotheratu.


Koma Mulungu analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake; Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake ndipo anayala thambo mwaluso lake.


Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo. Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse kuphatikizapo Israeli, mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake. Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.


Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka.


Uthenga wa Yehova kwa Israeli. Yehova, amene amayala mlengalenga, amene amayika maziko a dziko lapansi, ndiponso amene amalenga mzimu wokhala mwa munthu, akunena kuti,


Mwadzidzidzi gulu lalikulu la angelo linaonekera pamodzi ndi mngeloyo, kuyamika Mulungu ndi kumati,


Anthu atamva zimenezi anafuwula ndi mtima umodzi napemphera kwa Mulungu. Iwo anati, “Ambuye wolamulira zonse, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndiponso zonse zili mʼmenemo.


Koma Mulungu anawafulatira, nawapereka kuti apembedze zolengedwa zakumwamba. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la aneneri kuti, “ ‘Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?’


ndipo ngati motsutsana ndi lamulo langa wapembedza milungu ina, kuyigwadira milunguyo, kaya ndi dzuwa kapena mwezi kapena nyenyezi zakumwamba,


Ndipo pamene muyangʼana kumwamba muona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, zonse zakumwambazo musakopeke kuti muzigwadire ndi kumapembedza zinthu zimene Yehova wapereka kwa anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi.


Tsono ife amene takhulupirira talowa mu mpumulo, monga momwe Mulungu akunenera kuti, “Ndili wokwiya ndinalumbira kuti, ‘Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.’ ” Ananena zimenezi ngakhale anali atatsiriza kale ntchito yolenga dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa