Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 19:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Koma iye anawawumiriza kwambiri kotero kuti anapita naye pamodzi ku nyumba kwake. Anawakonzera chakudya buledi wopanda yisiti ndipo anadya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Loti adaumirirabe kuŵapempha, ndipo pambuyo pake iwo adavomera, napita kunyumba kwa Loti. Tsono Loti adaŵachitira phwando. Adaŵaphikira buledi wosafufumitsa naŵakonzera chakudya chokoma kwambiri, anthuwo nkudya.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 19:3
18 Mawu Ofanana  

Iye anati, “Ambuye wanga, chonde patukirani ku nyumba kwa mtumiki wanu. Mukhoza kusambitsa mapazi anu ndi kugona usiku uno kenaka nʼkumapitirira ndi ulendo wanu mmamawa.” Iwo anati, “Ayi, tigona panja.”


Mwana uja anakula mpaka kumuletsa kuyamwa. Tsiku lomuletsa Isake kuyamwa, Abrahamu anakonza phwando lalikulu.


Iye anati, “Tiyeni kwathu, ndinu munthu amene Yehova wamudalitsa. Bwanji mwangoyimirira panja pano? Ine ndakukonzerani malo ogona inu ndi ngamira zanu.”


Tsono Isake anawakonzera phwando, ndipo anadya ndi kumwa.


Tsiku lina Elisa anapita ku Sunemu. Kumeneko kunkakhala mayi wina wachuma amene anawumiriza Elisa kuti adye chakudya. Choncho nthawi iliyonse imene Elisa amadutsa kumeneko, ankayima ndi kudya.


Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti. Tsiku loyamba muzichotsa yisiti mʼnyumba zanu, ngati aliyense adzadya kanthu kalikonse kali ndi yisiti kuyambira tsiku loyamba mpaka tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzayenera kuchotsedwa mʼgulu la Israeli.


Iwo anapanga buledi wopanda yisiti ndi ufa umene anachoka nawo ku Igupto. Ufawo unalibe yisiti chifukwa anachita kuthamangitsidwa ku Igupto ndipo analibe nthawi yokonzera chakudya chawo.


Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna.


“Ndipo mbuye uja anawuza wantchito wake kuti, ‘Pita kunja ku misewu ikuluikulu ndi kunja kwa mpanda ndipo ukawawuze kuti alowe, kuti nyumba yanga idzaze.


Kenaka Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu ku nyumba yake ndipo gulu lalikulu la amisonkho ndi ena ankadya naye pamodzi.


Kumeneko anamukonzera Yesu chakudya cha madzulo. Marita anatumikira pamene Lazaro anali mmodzi wa iwo amene anakhala nawo pa chakudyacho.


Choncho, tiyeni tisunge chikondwererochi, osati ndi yisiti wakale, wowononga ndi woyipa, koma ndi buledi wopanda yisiti, buledi woona mtima ndi choonadi.


Pakuti chikondi cha Khristu ndicho chimatikakamiza, chifukwa tikutsimikiza kuti mmodzi anafera anthu onse, kotero kuti anthu onse anafanso.


Musayiwale kusamalira alendo, pakuti pochita zimenezi anthu ena anasamalira angelo amene samawadziwa.


Gideoni analowa mʼnyumba, ndipo anakakonza mwana wambuzi, nakonzanso makeke wopanda yisiti a ufa wa makilogalamu khumi. Nayika nyamayo mʼdengu ndipo msuzi wake anawuthira mu mʼphika. Anabwera nazo ndi kukazipereka kwa mngelo uja pa tsinde pa mtengo wa thundu paja.


Mkaziyo anali ndi mwana wangʼombe wonenepa ndipo anamupha mwachangu. Anatenga ufa nawukanyanga ndipo anaphika buledi wopanda yisiti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa