Genesis 12:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe, ndi kutemberera amene adzatemberera iwe; ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa iwe.” Onani mutuwoBuku Lopatulika3 ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 “Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe, koma ndidzatemberera aliyense wokutemberera. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.” Onani mutuwo |
Zitatha izi ndinayangʼana patsogolo panga ndipo ndinaona gulu lalikulu la anthu loti munthu sangathe kuliwerenga lochokera dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu wa anthu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse, atayima patsogolo pa mpando waufumu, pamaso pa Mwana Wankhosa. Iwo anali atavala mikanjo yoyera ndi kunyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo.