Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 12:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu ndipo ndidzakudalitsa; ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 12:2
38 Mawu Ofanana  

Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati fumbi lapansi moti amene angathe kuwerenga fumbilo ndiye kuti angathenso kuwerenga zidzukulu zako.


Yehova anapita naye Abramu panja nati, “Tayangʼana kumwambaku, ndipo chifukwa cha chimenechi uwerenge nyenyezi ngati ungathe kuziwerenga.” Ndipo anamuwuza kuti, “Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.”


Koma za Ismaeli, ndamva. Ndidzamudalitsadi, ndipo adzakhala ndi zidzukulu zambiri. Iye adzakhala kholo la mafumu khumi ndi awiri ndipo mwa iye mudzatuluka mtundu waukulu wa anthu.


Abrahamu adzakhaladi mtundu wa anthu waukulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya anthu pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa iye.


Pakuti ndasankha iyeyu kuti adzatsogolere ana ake ndi a pa banja lake, kuti asunge mawu a Yehova pochita zoyenera ndi zachilungamo. Choncho Yehova adzachita kwa Abrahamu chimene anamulonjeza iye.”


Choncho Mulungu anawononga mizinda ya ku chigwa, koma anakumbukira pemphero la Abrahamu natulutsa Loti ku sulufule ndi moto zimene zinawononga mizinda ya kumene Loti amakhalako.


Tsopano Abrahamu anali atakalamba kwambiri, ndipo Yehova anamudalitsa mu zonse anachita.


Yehova wadalitsa mbuye wanga kwambiri, ndiponso walemera. Wamupatsa nkhosa ndi ngʼombe, siliva ndi golide, antchito aamuna ndi antchito aakazi, komanso ngamira ndi abulu.


Atamwalira Abrahamu, Mulungu anadalitsa mwana wake Isake, amene ankakhala pafupi ndi Beeri-lahai-roi (chitsime cha Wamoyo Wondipenya).


Khala mʼdziko lino ndipo ndidzakhala nawe ndi kukudalitsa. Pakuti kwa iwe ndi zidzukulu zako ndidzapereka mayiko onsewa. Choncho ndidzakwaniritsa pangano limene ndinalumbira kwa Abrahamu, abambo ako.


Zidzukulu zako ndidzazichulukitsa ngati nyenyezi za mu mlengalenga ndi kuzipatsa mayiko onsewa. Ndiponso anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako,


Mitundu ya anthu ikutumikire iwe ndipo anthu akugwadire iwe. Ukhale wolamula abale ako, ndipo ana aamuna a amayi ako akugwadire. Amene akutemberera iwe atembereredwe ndipo amene adalitsa iwe adalitsike.”


Zidzukulu zako zidzachuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi ndipo zidzabalalikira kumadzulo ndi kummawa, kumpoto ndi kummwera. Anthu onse adzalandira madalitso kudzera mwa iwe ndi zidzukulu zako.


Ndipo Mulungu anati kwa iye, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse; berekanani ndi kuchulukana. Mtundu wa anthu, inde, mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe, ndipo ena mwa zidzukulu zako adzakhala mafumu.


Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu. Mulungu wa abambo ako. Usachite mantha kupita ku Igupto, pakuti ndidzachulukitsa zidzukulu zako kumeneko moti zidzakhala mtundu waukulu.


Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi.


Kuwonjezera pamenepo, nduna za mfumu zabwera kale kudzayamika mbuye wathu Mfumu Davide, pomanena kuti, ‘Mulungu wanu atchukitse dzina la Solomoni kuposa dzina lanu ndipo ufumu wake ukule kupambana ufumu wanu!’ Ndipo mfumu inawerama niyamba kupembedza pa bedi lake,


Kuyipa kwanu kumangokhudza anthu ngati inuyo, ndipo chilungamo chanu chimakhudza anthu anzanu.


Yehova anawadalitsa, ndipo chiwerengero chawo chinachuluka kwambiri, ndipo Iye sanalole kuti ziweto zawo zithe.


Koma Aisraeli anaberekana ndi kuchuluka kwambiri nakhala amphamvu kwambiri, kotero kuti anadzaza dzikolo.


Chifukwa chake undileke kuti mkwiyo wanga uyake pa iwo ndi kuwawononga. Ndipo Ine ndidzakusandutsa kuti ukhale mtundu waukulu.”


taganizani za Abrahamu, kholo lanu, ndi Sara, amene anakubalani. Pamene ndinkamuyitana nʼkuti alibe mwana, koma ndinamudalitsa ndi kumupatsa ana ambiri.


Ndidzakhazika anthu anga pafupi ndi phiri langa loyera ndipo ndidzawadalitsa. Ndidzawagwetsera mvula pa nthawi yake ndipo idzakhala mvula ya madalitso.


Mudzakhala wokhulupirika kwa Yakobo, ndi kuonetsa chifundo chanu kwa Abrahamu, monga munalonjeza molumbira kwa makolo athu masiku amakedzana.


Monga mwakhala muli chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu ina ya anthu, inu Yuda ndi Israeli, choncho ndidzakupulumutsani, ndipo mudzakhala dalitso. Musachite mantha, koma limbani mtima.”


Ndidzawakantha ndi mliri ndi kuwawononga. Koma ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu ndi wamphamvu kuposa iwo.”


Koma Mulungu anawuza Balaamu kuti, “Usapite nawo. Usawatemberere anthu amenewo chifukwa ndi odalitsika.”


Wandilamula kuti ndidalitse, Iyeyo wadalitsa ndipo sindingasinthe.


Ndipo iye anachita mdulidwe ngati chizindikiro ndi chitsimikizo cha kulungama kumene anali nako mwachikhulupiriro pomwe anali asanachite mdulidwe. Choncho, iye ndi kholo la onse amene akhulupirira koma sanachite mdulidwe, ndi cholinga chakuti alungamitsidwe.


Iye anatiwombola ife ndi cholinga chakuti madalitso woperekedwa kwa Abrahamu abwere kwa anthu a mitundu ina kudzera mwa Khristu Yesu, kuti ndi chikhulupiriro tilandire lonjezo la Mzimu.


Tsono zindikirani kuti amene akhulupirira, ndi ana a Abrahamu.


Ndipo mudzanenetsa pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, “Abambo anga anali Mwaramu woyendayenda, anapita ku Igupto ndi anthu ochepa nakhala kumeneko. Pambuyo pake anakhala mtundu waukulu, wamphamvu ndi wochuluka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa