Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 11:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Nthawi imeneyo anthu onse a pa dziko lapansi ankayankhula chiyankhulo chimodzi ndipo mawu amene ankayankhula anali amodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Poyambayamba anthu onse a pa dziko lapansi ankalankhula chilankhulo chimodzi, ndipo mau amene ankalankhulawo anali amodzi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 11:1
6 Mawu Ofanana  

Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.


Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako.


Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita.


Tsiku limenelo ku dziko la Igupto kudzakhala mizinda isanu yoyankhula chiyankhulo cha Akanaani, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti adzamutumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchedwa Mzinda Wachilungamo.


“Pamenepo ndidzayeretsa milomo ya anthu a mitundu yonse kuti anthu onsewo ayitane dzina la Yehova ndi kumutumikira Iye pamodzi.


Utamveka mkokomo uja, gulu la anthu linasonkhana. Anthuwo anadabwa chifukwa aliyense anawamva atumwiwo akuyankhula ziyankhulo zosiyanasiyana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa