Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Filemoni 1:21 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Ine ndili ndi chitsimikizo cha kumvera kwako pamene ndikukulembera kalatayi. Ndikulemba ndikudziwa kuti udzachita ngakhale kuposa zimene ndakupemphazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

21 Pokhulupirira kumvera kwako ndikulembera iwe, podziwa kuti udzachitanso koposa chimene ndinena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pokhulupirira kumvera kwako ndikulembera iwe, podziwa kuti udzachitanso koposa chimene ndinena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Ndikukulembera zimenezi, popeza kuti ndikukhulupirira kuti udzachitadi zimene ndakupempha. Ndikudziŵa kuti udzachita kopitiriranso zimene ndapemphazi.

Onani mutuwo Koperani




Filemoni 1:21
6 Mawu Ofanana  

ngati umadziwadi kuti ndiwe mtsogoleri wa osaona, nyale yowunikira amene ali mu mdima,


Nʼchifukwa chake ndinakulemberani monga ndinachitiramo kuti nditabwera kwanuko ndisadzamve chisoni ndi anthu oyenera kundisangalatsa. Ndinali ndi chikhulupiriro ndi inu nonse kuti inuyo mukakhala ndi chimwemwe poona kuti inenso ndili ndi chimwemwe.


Ndine wokondwa kuti ndingathe kukukhulupirirani pa zonse.


Kuwonjezera apo, tikuwatumiza pamodzi ndi mʼbale wathu, amene nthawi zambiri watitsimikizira mʼnjira zosiyanasiyana kuti ndi wachangu ndiponso chifukwa ali ndi chikhulupiriro chachikulu mwa inu.


Ine ndikutsimikiza mwa Ambuye kuti inu simudzasiyana nane maganizo. Iye amene akukusokonezani adzalangidwa, kaya iyeyo ndiye ndani.


Tili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye kuti mukuchita zonse ndipo mudzapitirira kuchita zimene tinakulamulirani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa