Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Filemoni 1:14 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, nʼcholinga chakuti chilichonse chabwino ungandichitire chikhale mwakufuna kwako osati mokakamiza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

14 koma wopanda kudziwa mtima wako sindinafune kuchita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 koma wopanda kudziwa mtima wako sindinafuna kuchita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, kuwopa kuti ungandichitire chinthu chabwinochi mokakamizidwa, osati mwaufulu.

Onani mutuwo Koperani




Filemoni 1:14
10 Mawu Ofanana  

Mulungu wanga, ine ndikudziwa kuti mumayesa mtima ndipo mumakondwera ndi anthu angwiro. Zinthu zonsezi ndapereka mwaufulu ndi cholinga chabwino. Ndipo tsopano ndaona ndi chimwemwe momwe anthu anu amene ali pano akuperekera mwaufulu kwa Inu.


Ankhondo ako adzakhala odzipereka pa tsiku lako la nkhondo. Atavala chiyero chaulemerero, kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha, udzalandira mame a unyamata wako.


Ngati ndikugwira ntchitoyi mwakufuna kwanga, ndili ndi mphotho; koma ngati si mwakufuna kwanga, ndiye kuti ntchitoyi ndi Ambuye anandipatsa.


Ndani angagwire ntchito ya usilikali namadzipezera yekha zofunika zonse? Kodi ndani amadzala mpesa koma wosadyako zipatso zake? Ndani amaweta nkhosa koma wosamwako mkaka wake?


Sikuti ife tikufuna kukhala olamulira chikhulupiriro chanu, koma timagwira nanu ntchito pamodzi kuti mukhale achimwemwe, chifukwa ndinu okhazikika kwambiri mʼchikhulupiriro.


Ndipo ngati mtima ofunitsitsa ulipo, mphatsoyo imalandiridwa molingana ndi zimene munthuyo ali nazo, osati zimene alibe.


Choncho ndinaganiza kuti nʼkofunika kupempha abale kuti adzakuchezereni ineyo ndisanafike, ndikuti adzatsirize kukonzekera mphatso zomwe munalonjeza kupereka mowolowamanja. Motero mphatsoyo idzakhala yokonzeratu, ndipo idzakhala mphatso yoperekedwa mowolowamanja, osati mokakamizidwa.


Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa