Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 9:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa Farao ndipo ukamuwuze kuti Yehova, Mulungu wa Ahebri akuti alole anthu anga apite kuti akandipembedze.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pambuyo pake Chauta adalamula Mose kuti, “Pita kwa Farao ukamuuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, akunena kuti uŵalole anthu anga apite akandipembedze.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 9:1
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kukanena kuti, “Yehova Mulungu wa Ahebri, akuti: ‘Kodi udzakanabe kudzichepetsa pamaso panga mpaka liti? Alole anthu anga apite kuti akandipembedze.


“Akuluakulu a Israeli akakumvera. Kenaka iwe ndi akuluakuluwo mukapite kwa mfumu ya Igupto ndipo mukanene kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri, wakumana nafe. Tsono tikukupemphani kuti mutilole tipite pa ulendo wa masiku atatu mʼchipululu kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’


Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ”


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Ukamuwuze Farao kuti, Lolani anthu anga kuti apite, akandipembedze.


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mmawa, upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso pamene azidzapita ku madzi ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Lola anthu anga kuti apite akandipembedze.


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mawa mmawa upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso ndipo ukamuwuze kuti Yehova Mulungu wa Ahebri akuti ulole anthu anga apite kuti akandipembedze.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa