Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 8:21 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Koma ngati suwalola anthu anga kuti apite, Ine ndidzatumiza pa iwe ntchentche zoluma ndi pa nduna zako ndi anthu ako ndi mʼnyumba zanu. Mʼnyumba za Aigupto mudzadzaza ntchentche zoluma. Ngakhale pa nthaka pamene akhalapo padzadzaza ndi ntchentche zoluma.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

21 Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aejipito zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aejipito zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Ukapanda kulola anthu anga kuti apite, ndidzatumiza mizaza pa iwe, nduna zako, anthu ako ndi m'nyumba mwako. M'nyumba zonse za Aejipito, ngakhalenso pa nthaka yonse imene akukhalapo, padzakhala mizaza yokhayokha.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 8:21
7 Mawu Ofanana  

Iye anayankhula, ndipo kunabwera ntchentche zochuluka ndi nsabwe mʼdziko lawo lonse.


Iye anawatumizira magulu a ntchentche zimene zinawawononga, ndiponso achule amene anawasakaza.


Dzombeli lidzadzaza nyumba zako ndi za nduna zako ndiponso za Aigupto onse, chinthu chimene ngakhale makolo anu kapena makolo awo sanachionepo kuyambira tsiku limene anakhala mʼdzikoli mpaka lero.’ ” Ndipo Mose ndi Aaroni anatembenuka ndi kumusiya Farao.


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mmawa, upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso pamene azidzapita ku madzi ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Lola anthu anga kuti apite akandipembedze.


“Koma pa tsikulo ndidzapatula dera la Goseni, kumene kumakhala anthu anga, motero kuti sikudzakhala ntchentche zoluma. Choncho iwe udzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndikulamulira dziko lino.


Ndipo Yehova anachita zimenezi: Ntchentche zoluma zochuluka zinalowa mʼnyumba yaufumu ya Farao ndi nyumba za nduna zake. Choncho ntchentche zolumazi zinawononga dziko lonse la Igupto.


Tsiku limenelo Yehova adzalizira likhweru ntchentche zochokera ku mitsinje yakutali ku Igupto, ndiponso njuchi zochokera ku dziko la Asiriya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa