Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 8:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Achule adzachoka mʼnyumba yanu, mʼnyumba za nduna zanu pamodzi ndi za anthu anu. Koma adzatsala mu mtsinje wa Nailo basi.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

11 Ndipo achule adzachokera inu, ndi nyumba zanu, ndi anyamata anu, ndi anthu anu; adzatsala m'mtsinje mokha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo achule adzachokera inu, ndi nyumba zanu, ndi anyamata anu, ndi anthu anu; adzatsala m'nyanja mokha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Achulewo adzakuchokani, adzachokanso m'nyumba zanu, m'nyumba za nduna zanu, ndipo azidzangokhala mumtsinje mokha.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 8:11
7 Mawu Ofanana  

Yehova anati kwa Mose, “Ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao zodabwitsa zonse zimene ndayika mphamvu mwa iwe kuti ukachite. Koma Ine ndidzawumitsa mtima wake kotero kuti sadzalola anthuwo kuti apite.


Koma mtima wa Farao unawuma ndipo sanawamvere monga momwe Yehova ananenera.


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Farao ndi wowuma mtima. Akukana kulola anthu anga kuti apite.


Mose ndi Aaroni anachoka, ndipo Mose anapemphera kwa Yehova kuti achotse achule amene anatumiza kwa Farao.


Ndipo Yehova anachita zomwe Mose anapempha. Achule amene anali mʼnyumba, mʼmabwalo ndi mʼminda anafa


Mtsinje wa Nailo udzadzaza ndi achule. Achulewo adzatuluka ndi kukalowa mʼnyumba yaufumu, ku chipinda chogona ndi pa bedi lako, mʼnyumba za nduna zako ndi pa anthu ako ndi mophikira buledi ndiponso mopangira bulediyo.


Mose anati kwa Farao, “Inu mungonditchulira nthawi imene mukufuna kuti ndikupempherereni, nduna zanu pamodzi ndi anthu anu kuti achule achoke mʼnyumba zanu ndi kuti atsale okhawo ali mu mtsinje wa Nailo.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa