Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 7:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndipo Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzatambasula dzanja langa kukantha Igupto ndi kutulutsa Aisraeli mʼdzikomo.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aejipito, ndikutulutsa ana a Israele pakati pao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aejipito, ndikutulutsa ana a Israele pakati pao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Apo Aejipito adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaŵakantha ndi dzanja langa ndi kutulutsa Aisraele m'dziko mwaomo.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 7:5
20 Mawu Ofanana  

Ngakhale ndiyende pakati pa masautso, mumasunga moyo wanga; mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga, mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.


Yehova amadziwika ndi chilungamo chake; oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo. Higayoni. Sela


kuti inu mudzawuze ana ndi zidzukulu zanu za mmene ndinawakhawulitsira Aigupto ndi zizindikiro zozizwitsa zimene ndinachita pakati pawo ndiponso kuti inu mudziwe kuti ine ndine Yehova.”


Nduna za Farao zinamufunsa kuti, “Kodi munthu uyu adzativutitsa mpaka liti? Aloleni anthuwa apite, kuti akapembedze Yehova Mulungu wawo. Kodi simukuona kuti dziko la Igupto lawonongeka?”


Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova akadzaona mmene ndipambanire Farao ndi magaleta ndi owayendetsa ake.”


Ndidzawumitsa mtima wa Farao ndipo adzathamangira Aisraeliwo. Choncho ndikadzagonjetsa Farao ndi gulu lake lonse la nkhondo, Ine ndidzalemekezedwa.” Choncho Aisraeli aja anachita zimenezi.


Mose anafotokozera mpongozi wake zonse zimene Yehova anamuchita Farao ndi Aigupto chifukwa cha Israeli komanso zowawa zonse anakumana nazo mʼnjira. Mose anafotokozanso momwe Yehova anawapulumutsira.


Tsono Ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kukantha Aigupto ndi zodabwitsa zanga zimene ndidzazichita pakati pawo. Zikadzatha izi, Iye adzakulolani kuti mupite.


Yehova anawuza Mose kuti, “Tsopano udzaona zimene ndimuchite Farao: Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzalola anthu anga kuti atuluke. Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzawatulutsa mʼdziko lake.”


“Nʼchifukwa chake nena kwa Aisraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani mʼgoli la Aigupto. Ndidzakumasulani mu ukapolo, ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasuka ndi kuchita ntchito zachiweruzo.


Izi ndi zimene Yehova akunena: Ndi ndodo imene ili mʼdzanja langa ndidzamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi adzasanduka magazi. Ndikadzachita ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova:


Farao anati, “Mawa.” Mose anamuyankha kuti, “Chabwino zidzakhala monga mwaneneramu, kuti mudzadziwe kuti palibe wina wofanana ndi Yehova Mulungu wathu.


Amatsenga anati kwa Farao, “Izi wachita ndi Mulungu.” Koma mtima wa Farao unali wowumabe ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananenera.


“Koma pa tsikulo ndidzapatula dera la Goseni, kumene kumakhala anthu anga, motero kuti sikudzakhala ntchentche zoluma. Choncho iwe udzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndikulamulira dziko lino.


Ndidzawabwezera chilango choopsa ndipo ndidzawalanga mu mkwiyo wanga. Ndikadzawalipsira ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”


‘Ine Ambuye Yehova ndikuti, “ ‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni, ndipo ndidzalemekezedwa chifukwa cha iwe. Anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova ndikadzakulanga ndi kudzionetsa kuti ndine woyera pakati pako.


Ndikadzasandutsa dziko la Igupto kukhala bwinja; ndikadzawononga dziko lonse ndi kukantha onse okhala kumeneko, adzadziwa kuti ndine Yehova.’


Ndidzaonetsa chiyero cha dzina langa lotchuka, limene layipitsidwa pakati pawo. Anthu a mitundu inayo atadzazindikira kuti ndaonetsa kudzera mwa inu kuti dzina langa ndi loyera, iwo adzadziwanso kuti Ine ndine Yehova. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.


Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo Aisraeli adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.


“Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Israeli. Sindidzalola kuti dzina langa liyipitsidwenso, ndipo mitundu ya anthu idzadziwa kuti Ine Yehova ndine Woyera mu Israeli.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa