Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 7:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 iyeyo sadzakumverani. Choncho ndidzakantha Igupto, ndipo ndi ntchito zachiweruzo ndidzatulutsa magulu anga, anthu anga Aisraeli kuwachotsa mʼdziko la Igupto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aejipito, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israele, m'dziko la Ejipito ndi maweruzo aakulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aejipito, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israele, m'dziko la Ejipito ndi maweruzo akulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Faraoyo sadzakumverani. Pamenepo ndidzakantha dzikolo, ndipo pochita ntchito zamphamvu, ndidzatsogolera magulu anga, anthu anga Aisraele, kuŵatulutsa ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 7:4
28 Mawu Ofanana  

Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa Farao, pakuti Ine ndawumitsa mtima wake ndi mitima ya nduna zake kuti ndichite zizindikiro zozizwitsa pakati pawo


Yehova ananena kwa Mose kuti, “Farao adzakana kukumvera, kuti zodabwitsa zanga zichuluke mʼdziko la Igupto.”


Ndipo tsiku lomwelo Yehova anatulutsa gulu lonse la ana a Israeli mʼdziko la Igupto.”


Ndipo Mose anati kwa anthu, “Muzikumbukira tsiku lino, tsiku limene munatuluka mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo chifukwa Yehova anakutulutsani ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye kalikonse kamene kali ndi yisiti.


Lamulo ili lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi chikumbutso choyikidwa pamphumi panu kuti malamulo a Yehova asachoke pakamwa panu. Pakuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu.


Mose anafotokozera mpongozi wake zonse zimene Yehova anamuchita Farao ndi Aigupto chifukwa cha Israeli komanso zowawa zonse anakumana nazo mʼnjira. Mose anafotokozanso momwe Yehova anawapulumutsira.


Koma Ine ndikudziwa kuti mfumu ya Igupto sikakulolani kuti mupite pokhapokha Ine nditayikakamiza.


Tsono Ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kukantha Aigupto ndi zodabwitsa zanga zimene ndidzazichita pakati pawo. Zikadzatha izi, Iye adzakulolani kuti mupite.


Yehova anawuza Mose kuti, “Tsopano udzaona zimene ndimuchite Farao: Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzalola anthu anga kuti atuluke. Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzawatulutsa mʼdziko lake.”


Aaroni ndi Mose ndi aja amene Yehova anawawuza kuti, “Tulutsani Aisraeli mu Igupto mʼmagulu awo.”


“Nʼchifukwa chake nena kwa Aisraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani mʼgoli la Aigupto. Ndidzakumasulani mu ukapolo, ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasuka ndi kuchita ntchito zachiweruzo.


Koma mtima wa Farao unawuma ndipo sanawamvere monga momwe Yehova ananenera.


Ndipo ukamuwuze Farao kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri wandituma kuti ndikuwuzeni kuti: Lolani anthu anga apite kuti akandipembedze mʼchipululu. Koma mpaka tsopano inu simunandimvere.


Koma Farao ataona kuti zinthu zinayambanso kukhala bwino, anawumitsanso mtima wake ndipo sanamverenso mawu a Mose ndi Aaroni, monga momwe Yehova ananenera.


Amatsenga anati kwa Farao, “Izi wachita ndi Mulungu.” Koma mtima wa Farao unali wowumabe ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananenera.


Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo iye sanamvere Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova anamuwuzira Mose.


dzanja la Yehova lidzakantha ziweto zako zimene zili ku munda, pamodzi ndi akavalo, abulu, ngamira, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi ndi mliri woopsa kwambiri.


Chilango chakonzedwa kale kuti chigwere anthu oyipa, ndipo mkwapulo wakonzedwa kale kuti ukwapule misana ya anthu opusa.


Moyo wanga umalakalaka Inu usiku wonse; nthawi yammawa ndimafunafuna Inu. Pamene muweruza dziko lapansi anthu amaphunzira kuchita chilungamo.


zoonadi anandikantha ndi dzanja lake mobwerezabwereza tsiku lonse.


“Pakuti Ambuye Yehova akuti: Kudzakhala zoopsa kwambiri pamene ndidzatumiza pa Yerusalemu zilango zanga zinayi izi: lupanga, njala, zirombo ndi mliri kuti ziwononge anthu ake ndi nyama zomwe!


Ndidzawalangadi Amowabuwo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”


Ndidzasandutsa chipululu mzinda wa Patirosi, ndi kutentha mzinda wa Zowani. Ndidzalanga mzinda wa Thebesi.


Kotero ndidzalanga dziko la Igupto, ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”


Inu Ambuye, ndani angapande kukuopani, ndi kulemekeza dzina lanu? Pakuti Inu nokha ndiye woyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzapembedza pamaso panu, pakuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”


Kenaka ndinamva mawu ochokera ku guwa lansembe akuti, “Inde, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, chiweruzo chanu ndi choona ndi cholungama.”


pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake. Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.”


Nthawi zonse Aisraeli ankati akapita ku nkhondo, Yehova amalimbana nawo kuti agonjetsedwe, monga ananenera molumbira kuti zidzaterodi. Choncho iwo anali pa mavuto aakulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa