Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 7:22 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Koma amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. Choncho Farao anawumabe mtima, ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananeneratu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

22 Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Tsono amatsenga a ku Ejipito aja nawonso adachita zomwezo mwa matsenga ao, ndipo Farao adakhalabe wokanika. Sadamvere zimene ankanena Mose ndi Aroni monga momwe Chauta adaanenera muja.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 7:22
8 Mawu Ofanana  

Mmawa, Farao anavutika mu mtima kotero anayitanitsa amatsenga ndi anzeru onse a mu Igupto. Iwo atabwera, iye anawawuza maloto ake, koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kutanthauzira malotowo kwa Farao.


Naye Farao anayitanitsa anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo nawonso amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo.


Koma mtima wa Farao unawuma ndipo sanawamvere monga momwe Yehova ananenera.


Nsomba za mu Nailo zinafa ndipo mtsinje unanunkha kwambiri kotero kuti Aigupto sanathe kumwa madzi ake. Magazi anali ponseponse mu Igupto.


Mʼmalo mwake iye anatembenuka ndi kupita ku nyumba yake yaufumu ndipo zimenezi sanazilabadire.


Ngati iwo ndi aneneri ndipo ali ndi mawu a Yehova, apempheretu kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti ziwiya zimene zatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndiponso mu Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babuloni.


Monga momwe Yanesi ndi Yambere anawukira Mose, momwemonso anthu amenewa amawukira choonadi. Nzeru zawo ndi zowonongeka ndipo pa za chikhulupiriro, ndi okanidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa