Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 6:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndamvanso kubuwula kwa Aisraeli, amene Aigupto awayesa akapolo ndipo ndakumbukira pangano langa.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Ndamvanso kubuula kwa ana a Israele, amene Aejipito awayesa akapolo; ndipo ndakumbukira chipangano changa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndamvanso kubuula kwa ana a Israele, amene Aejipito awayesa akapolo; ndipo ndakumbukira chipangano changa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsopano ndamva kudandaula kwa Aisraele, amene ali mu ukapolo wa Aejipito, ndipo ndakumbukira chipangano changa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 6:5
11 Mawu Ofanana  

Tsono Mulungu anakumbukira Nowa ndi nyama zonse zakuthengo ndi ziweto zimene anali nazo mu chombo. Yehova anatumiza mphepo pa dziko lapansi ndipo madzi anaphwera.


ndizikumbukira pangano langa pakati pa Ine ndi inu ndi zolengedwa zonse. Madzi sadzakhalanso chigumula chowononga dziko lapansi.


Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya, mawu amene analamula kwa mibado yonse,


Nthawi yonseyo nʼkuti ana a Israeli akulira chifukwa cha ukapolo wawo uja. Iwo anafuwula kupempha thandizo, ndipo kulira kwawoko kunafika kwa Mulungu.


Mulungu anamva kubuwula kwawo ndipo anakumbukira pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo.


Yehova anati, “Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo chifukwa cha anthu amene akuwapsinja, ndipo ndakhudzidwa ndi masautso awo.


Koma mfumu ya Igupto inati, “Mose ndi Aaroni, chifukwa chiyani mukuchititsa anthuwa kuti asagwire ntchito zawo? Bwererani ku ntchito zanu!”


Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse, ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa. Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa, anawanyamula ndikuwatenga kuyambira kale lomwe.


Iye anathandiza mtumiki wake Israeli, pokumbukira chifundo chake.


kuonetsa chifundo kwa makolo athu ndi kukumbukira pangano lake loyera,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa