Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 6:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mayina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zawo anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Levi anakhala ndi moyo kwa zaka 137.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Ndipo maina a ana aamuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo maina a ana amuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Maina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zao naŵa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Leviyo adakhala zaka 137 ali moyo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 6:16
22 Mawu Ofanana  

Isake anakhala ndi moyo zaka 180.


Ana aamuna a Levi ndi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.


Ana aamuna a Rubeni ndi awa: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi.


Yakobo anakhala ku Igupto zaka 17 ndipo zaka za moyo wake zinali 147.


Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto.


Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.


Ana a Levi anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.


Ana a Levi anali awa: Geresomu, Kohati ndi Merari.


Ndipo Alevi awa anakonzeka kugwira ntchito: Kuchokera ku banja la Kohati, Mahati mwana wa Amasai ndi Yoweli mwana wa Azariya; kuchokera ku banja la Merari, Kisi mwana wa Abidi ndi Azariya mwana wa Yehaleleli; kuchokera ku banja la Geresoni, Yowa mwana wa Zima ndi Edeni mwana wa Yowa;


Ndipo munthu wina wa fuko la Levi anakwatira mkazi wa fuko lomwelo.


Ana a Kohati anali Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Kohati anakhala ndi moyo zaka 133.


Amramu anakwatira Yokobedi mlongo wa abambo ake, amene anabereka Aaroni ndi Mose. Amramu anakhala ndi moyo kwa zaka 137.


Kora mwana wa Izihari, mwana wa Kohati, mwana wa Levi ndi Datani ndi Abiramu ana a Eliabu, pamodzi ndi Oni mwana wa Perezi, ana a Rubeni, anayamba kudzikuza,


Alevi omwe anawerengedwa monga mwa mafuko awo ndi awa: kuchokera mwa Geresoni, fuko la Ageresoni; kuchokera mwa Kohati, fuko la Akohati; kuchokera mwa Merari, fuko la Amerari.


Mayina a ana aamuna a Levi ndi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.


Mayina a ana a Geresoni potsata mabanja awo ndi awa: Libini ndi Simei.


Ana a Kohati potsata mabanja awo ndi awa: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.


Ana a Merari potsata mabanja awo ndi awa: Mali ndi Musi. Amenewa ndiwo anali mabanja a Alevi monga mwa makolo awo.


Kwa Geresoni kunali banja la Alibini, banja la Asimei. Amenewa ndiwo anali mabanja a Ageresoni.


Maere oyamba anagwera mabanja a Kohati, Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aaroni anapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini.


Zidzukulu za Geresoni zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mabanja a mafuko a Isakara, Aseri, Nafutali ndi theka la fuko la Manase ku Basani.


ochokera fuko la Simeoni analipo 12,000; ochokera fuko la Levi analipo 12,000; ochokera fuko la Isakara analipo 12,000;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa