Eksodo 5:21 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 ndipo iwo anati, “Yehova akupenyeni ndi kukuweruzani popeza mwachititsa Farao ndi nduna zake kuti anyansidwe nafe ndipo mwayika lupanga mʼmanja mwawo kuti atiphe.” Onani mutuwoBuku Lopatulika21 ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 ndipo adaŵauza kuti, “Chauta aone mwachitazi, ndipo akuweruzeni inu poti Farao ndi nduna zake mwaŵasandutsa adani athu. Inuyo ndinu amene mwaika lupanga m'manja mwao kuti atiphe ife.” Onani mutuwo |
“Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu, kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu, gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawa ndi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo. Ndipo mitembo yawo idzawola, fungo lake lidzamveka.” Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.