Eksodo 4:22 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Ndipo iwe ukati kwa Farao, ‘Yehova akuti, Israeli ali ngati mwana wanga wachisamba.’ Onani mutuwoBuku Lopatulika22 Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Ndipo ukamuuze Farao kuti, Ine Chauta ndikuti Israele ali ngati mwana wanga wachisamba. Onani mutuwo |
“Mwana amalemekeza abambo ake, ndipo wantchito amaopa abwana ake. Ngati Ine ndine abambo anu, ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiopa kuli kuti?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndinu, inu ansembe, amene mumanyoza dzina langa. “Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi timanyoza dzina lanu bwanji?’