Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 4:21 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Yehova anati kwa Mose, “Ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao zodabwitsa zonse zimene ndayika mphamvu mwa iwe kuti ukachite. Koma Ine ndidzawumitsa mtima wake kotero kuti sadzalola anthuwo kuti apite.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

21 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Chauta adauzanso Mose kuti, “Pamene ukubwerera ku Ejipito, ukachite ndithu pamaso pa Farao zozizwitsa zonse zimene ndakuuza kuti ukachite. Koma ndidzamuumitsa mtima, ndipo sadzalola kuti anthu anga apite.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 4:21
34 Mawu Ofanana  

Tsono Yehova anati, “Sindilola kuti chipwirikiti chikuchitikachi chipitirire mpaka muyaya, pakuti iye ndi munthu; masiku a moyo wake adzakhala zaka 120.”


Yehova anafunsa kuti, “Ukamukopa bwanji?” Mzimuwo unati, “Ndidzapita ndi kukakhala mzimu wabodza pakamwa pa aneneri ake onse.” Yehova anati, “ ‘Iwe udzamukopadi. Pita kachite zomwezo.’


amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake, kukonzera chiwembu atumiki ake.


tsiku limene Iyeyo anaonetsa poyera zizindikiro zozizwitsa zake mu Igupto, zozizwitsa zake mʼchigawo cha Zowani.


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa Farao, pakuti Ine ndawumitsa mtima wake ndi mitima ya nduna zake kuti ndichite zizindikiro zozizwitsa pakati pawo


Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli apite.


Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo sanafune kuwalola kuti apite.


Mose ndi Aaroni anachita zodabwitsa zonsezi pamaso pa Farao koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli atuluke mʼdziko lake.


Yehova ananena kwa Mose kuti, “Farao adzakana kukumvera, kuti zodabwitsa zanga zichuluke mʼdziko la Igupto.”


Ine ndidzawumitsa mitima ya Aigupto kotero kuti adzatsatirabe Aisraeli. Ndipo ine ndikadzagonjetsa Farao ndi asilikali ake onse ankhondo, okwera magaleta ndi akavalo, ndidzapeza ulemerero.


Ndidzawumitsa mtima wa Farao ndipo adzathamangira Aisraeliwo. Choncho ndikadzagonjetsa Farao ndi gulu lake lonse la nkhondo, Ine ndidzalemekezedwa.” Choncho Aisraeli aja anachita zimenezi.


Yehova anawumitsa mtima wa Farao mfumu ya dziko la Igupto, kotero iye anawathamangira Aisraeli amene ankachoka mʼdzikomo mosavutika.


Koma Ine ndikudziwa kuti mfumu ya Igupto sikakulolani kuti mupite pokhapokha Ine nditayikakamiza.


Tsono Ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kukantha Aigupto ndi zodabwitsa zanga zimene ndidzazichita pakati pawo. Zikadzatha izi, Iye adzakulolani kuti mupite.


Koma mtima wa Farao unawuma ndipo sanawamvere monga momwe Yehova ananenera.


Koma ndidzawumitsa mtima wa Farao, ndipo ngakhale nditachulukitsa zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa mu Igupto,


Achule adzachoka mʼnyumba yanu, mʼnyumba za nduna zanu pamodzi ndi za anthu anu. Koma adzatsala mu mtsinje wa Nailo basi.”


Koma Farao ataona kuti zinthu zinayambanso kukhala bwino, anawumitsanso mtima wake ndipo sanamverenso mawu a Mose ndi Aaroni, monga momwe Yehova ananenera.


Koma nthawi imeneyinso Farao anawumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti anthu atuluke.


Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo iye sanamvere Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova anamuwuzira Mose.


Choncho Farao sanalole kuti Aisraeli apite monga momwe Yehova anamuwuzira Mose.


Tsono anthu amenewa uwaphe mtima; uwagonthetse makutu, ndipo uwatseke mʼmaso. Mwina angaone ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi mitima yawo, kenaka ndi kutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.”


Chifukwa chiyani, Inu Yehova, mukutisocheretsa pa njira zanu? Bwanji mukutilola kuti tikhale owuma mitima kotero kuti sitikukuopaninso? Bwererani chifukwa cha atumiki anu; mafuko a anthu amene ali cholowa chanu.


“Iye wachititsa khungu maso awo ndi kuwumitsa mitima yawo, kotero kuti iwo sangathe kuona ndi maso awo, kapena kuzindikira ndi mitima yawo, kapena kutembenuka kuti Ine ndikanawachiza.”


Ndipo popeza anaona kuti nʼchopanda nzeru kumvera Mulungu, Iye anawasiya kuti atsatire maganizo achitayiko kuti achite zosayenera kuchitazo.


Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.


Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi?


Kuchokera ku Aroeri mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni ndi ku mzinda wa ku mtsinjeko mpaka kukafika ku Giliyadi, panalibe ndi mzinda ndi umodzi omwe umene unatikanika kuwugonjetsa. Yehova Mulungu wathu anatipatsa onsewo.


Yehova anali atawumitsa mitima yawo kuti alimbane ndi Aisraeli kuti aphedwe popanda kuchitiridwa chifundo. Izi ndi zimene Yehova analamula Mose kuti zichitidwe.


ndi “Mwala wopunthwitsa anthu ndiponso thanthwe limene limagwetsa anthu.” Iwo amapunthwa chifukwa samvera uthenga, pakuti ichi ndiye chinali chifuniro cha Mulungu pa iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa