Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 39:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Iwo anapanga chovala chapachifuwa mwaluso kwambiri. Anachipanga ngati efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala ndi yolukidwa bwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Ndipo anaomba chapachifuwa, ntchito ya mmisiri, monga maombedwe ake a efodi; cha golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo anaomba chapachifuwa, ntchito ya mmisiri, monga maombedwe ake a efodi; cha golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Pambuyo pake adapanga chovala chapachifuwa mwaluso kwambiri, monga chovala cha efodi chija. Adachipanga ndi nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira, ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 39:8
9 Mawu Ofanana  

Ndidzamusungira chifundo changa kwamuyaya, ndipo pangano langa ndi iye silidzatha.


miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa efodi ndi pa chovala cha pachifuwa.


“Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi.


Zovala zoti apange ndi izi: chovala chapachifuwa, efodi, mkanjo, mwinjiro wolukidwa, nduwira ndi lamba. Apangire mʼbale wako Aaroni ndi ana ake aamuna zovala zopatulikazi kuti iwo anditumikire monga ansembe.


Kutalika kwake kunali kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, chinali chopinda pawiri.


Iye anavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa, ndipo kumutu kwake amavala chipewa chachipulumutso; anavala kulipsira ngati chovala ndipo anadzikuta ndi mkwiyo ngati chofunda.


Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa