Eksodo 33:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Pitani ku dziko loyenda mkaka ndi uchi. Koma ine sindidzapita nanu, chifukwa anthu inu ndinu nkhutukumve ndipo nditha kukuwonongani mʼnjiramo.” Onani mutuwoBuku Lopatulika3 kudziko koyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, pakuti sindidzakwera pakati pa inu; popeza inu ndinu anthu opulupudza; ndingathe inu panjira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 kudziko koyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, pakuti sindidzakwera pakati pa inu; popeza inu ndinu anthu opulupudza; ndingathe inu panjira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Pitani ku dziko lamwanaalirenji. Koma Ine sindidzapita nanu chifukwa ndinu anthu okanika, ndipo ndingathe kukuwonongani panjira.” Onani mutuwo |
Aisraeli anakhala akuyenda mʼchipululu kwa zaka makumi anayi mpaka amuna onse amene potuluka mʼdziko la Igupto anali a msinkhu woyenera kupita ku nkhondo anamwalira. Iwo anafa chifukwa sanamvere mawu a Yehova. Yehova anawalumbirira kuti sadzalowa konse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi limene analonjeza kwa makolo awo kuti adzatipatsa.