Eksodo 32:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Koma Mose anapempha chifundo cha Mulungu wake ndipo anati, “Chonde Yehova, chifukwa chiyani mwakwiyira anthu awa amene munawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi mphamvu yanu yayikulu ndi dzanja lanu lamphamvu. Onani mutuwoBuku Lopatulika11 Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Koma Mose adapepesa Chauta wake, nati, “Inu Chauta, chifukwa chiyani mukukwiyira anthu anu chotere, anthu amene mudaŵatulutsa mu ukapolo ku Ejipito kuja ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lamphamvu? Onani mutuwo |
Ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova, alire pakati pa guwa lansembe ndi khonde la Nyumba ya Yehova. Azinena kuti, “Inu Yehova, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti cholowa chanu chikhale chinthu chonyozeka, kuti anthu a mitundu ina awalamulire. Kodi nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina amanena kuti, ‘Ali kuti Mulungu wawo?’ ”