Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 32:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Chifukwa chake undileke kuti mkwiyo wanga uyake pa iwo ndi kuwawononga. Ndipo Ine ndidzakusandutsa kuti ukhale mtundu waukulu.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Nchifukwa chake tsono, undileke kuti ndiŵaononge chifukwa ndili wokwiya kwambiri, koma iweyo ndidzakusandutsa mtundu waukulu wa anthu.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 32:10
21 Mawu Ofanana  

“Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu ndipo ndidzakudalitsa; ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.


Choncho Iye anawawuza kuti adzawawononga, pakanapanda Mose, mtumiki wake wosankhidwa, kuyima pamaso pake, ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usawawononge.


Ine ndidzakukwiyirani ndipo ndidzakuphani ndi lupanga. Akazi anu adzakhala amasiye ndiponso ana anu adzakhala wopanda abambo.


Koma Mose anapempha chifundo cha Mulungu wake ndipo anati, “Chonde Yehova, chifukwa chiyani mwakwiyira anthu awa amene munawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi mphamvu yanu yayikulu ndi dzanja lanu lamphamvu.


Mose atayandikira msasa ndi kuona mwana wangʼombe ndiponso kuvina, anakwiya kwambiri ndipo anaponya pansi miyala imene inali mʼmanja mwake, ndi kuyiphwanya pa tsinde la phiri.


Pitani ku dziko loyenda mkaka ndi uchi. Koma ine sindidzapita nanu, chifukwa anthu inu ndinu nkhutukumve ndipo nditha kukuwonongani mʼnjiramo.”


“Tsono iwe Yeremiya usawapempherere anthu amenewa ngakhale kuwadandaulira kapena kuwapepesera, chifukwa sindidzawamvera akadzandiyitana pa nthawi ya mavuto awo.


Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Usawapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino.


Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samueli akanayima pamaso panga kupempherera anthu awa, Ine sindikanawachitira chisoni. Achotseni ndipo ndisawaonenso! Aleke apite!


“Choncho iwe Yeremiya usawapempherere anthu awa ngakhale kuwapepesera kapenanso kuwapembedzera; usandidandaulire, chifukwa Ine sindidzakumvera.


“ ‘Komabe anthu a Israeli anandiwukira mʼchipululu. Iwo sanatsatire malangizo anga koma anakana malamulo anga amene munthu aliyense akawamvera adzakhala ndi moyo. Ndipo anayipitsa kotheratu Masabata anga. Choncho, ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawononga mʼchipululu.


Ndidzawakantha ndi mliri ndi kuwawononga. Koma ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu ndi wamphamvu kuposa iwo.”


“Chokani pakati pa gulu ili kuti ndithetse mkanganowu kamodzinʼkamodzi.”


Koma Mose ndi Aaroni anadzigwetsa chafufumimba ndipo analira mokweza, “Chonde Mulungu, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, kodi mudzakwiyira gulu lonse pamene munthu mmodzi yekha ndiye amene wachimwa?”


Ndilekeni ndiwawononge ndi kufafaniza mayina awo pa dziko lapansi. Ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu wa anthu wamphamvu ndi wochuluka kuposa iwo.”


Ine ndinachita mantha ndi mkwiyo ndi ukali wa Yehova chifukwa anakwiya nanu kokwanira kukuwonongani. Koma Yehova anandimveranso.


Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa