Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 3:15 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Mulungu anatinso kwa Mose, “Ukanene kwa Aisraeli kuti ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo, wandituma kwa inu.’ Ili ndilo dzina langa mpaka muyaya, ndipo mibado ya mʼtsogolomo izidzanditchula ndi dzina limeneli.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

15 Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Ndipo Mulungu adamuuzanso Mose kuti, “Aisraele ukaŵauze kuti, Chauta, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe, ndiye amene wandituma kwa inu. Tsono limeneli ndilo dzina langa mpaka muyaya. Limeneli ndilo dzina limene idzanditchula mibadwo yonse yam'tsogolo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 3:15
41 Mawu Ofanana  

Ndipo wantchito uja anapemphera nati, “Haa, Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, mulole kuti zinthu zindiyendere ine lero, ndipo muonetseni mbuye wanga Abrahamu kukoma mtima kwanu kosasinthika.


pangano limene anachita ndi Abrahamu, lonjezo limene analumbira kwa Isake.


Inu Yehova Mulungu wa makolo athu Abrahamu, Isake ndi Israeli, mukhazikitse chofuna ichi mʼmitima ya anthu anu kwamuyaya, ndipo mukhazikitse mtima wokhulupirika kwa Inu.


Koma kumeneko kunali mneneri wa Yehova dzina lake Odedi, ndipo anapita kukakumana ndi gulu lankhondo pamene linabwerera ku Samariya. Iye anawawuza kuti, “Chifukwa Yehova, Mulungu wa makolo anu anakwiyira Ayuda, Iye anawapereka mʼdzanja lanu. Koma inu mwawapha mwaukali, ukali wake wofika mpaka kumwamba.


Koma Inu Yehova, muli pa mpando wanu waufumu kwamuyaya; kudziwika kwanu ndi kokhazikika ku mibado yonse.


Inu mudzadzuka ndi kuchitira chifundo Ziyoni pakuti ndi nthawi yoti muonetse kukoma mtima kwanu pa iyeyo; nthawi yoyikika yafika.


Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya, mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse.


Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika; tamandani dzina lake loyera.


Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse; utha kuchezera kulira usiku wonse, koma chimwemwe chimabwera mmawa.


Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye, ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.


Dzina lake likhazikike kwamuyaya, lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa. Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye ndipo iwo adzamutcha iye wodala.


Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake. Ameni ndi Ameni.


Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamutamanda, Mulungu wa makolo anga, ine ndidzamukweza.


Yehova ndi wankhondo; Yehova ndilo dzina lake.


Mose anati kwa Mulungu, “Ngati ndipita kwa Aisraeli ndi kukawawuza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ ndipo iwo nʼkukandifunsa kuti ‘Dzina lake ndi ndani?’ Tsono ine ndikawawuze chiyani?”


Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.” Atamva zimenezi, Mose anaphimba nkhope yake chifukwa anaopa kuona Mulungu.


Mose anayankha, “Aisraeliwo sakandikhulupirira ndipo sakandimvera. Iwowo adzati, ‘Yehova sanakuonekere iwe.’ ”


Yehova anati, “Ukachite zimenezi ndipo akakukhulupirira kuti Yehova, Mulungu wa makolo awo, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo, wakuonekera iwe.”


Mulungu anatinso kwa Mose, “Ine ndine Yehova.


Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba; wolungama amathawiramo napulumuka.


Inde Yehova, timayenda mʼnjira zanu zolungama, ife timayembekezera Inu; mitima yathu imakhumba kukumbukira ndi kulemekeza dzina lanu.


“Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo! Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense kapena matamando anga kwa mafano.


Ali kuti amene anachita zinthu zodabwitsa ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose? Ali kuti amene anagawa madzi pa nyanja anthu ake akuona, kuti dzina lake limveke mpaka muyaya,


Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife, ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake. Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.


“Yehova amene analenga dziko lapansi, kuliwumba ndi kulikhazikitsa; amene dzina lake ndi Yehova, akuti,


Ndikuyamika ndi kutamanda Inu Mulungu wa makolo anga: mwandipatsa nzeru ndi mphamvu, mwandiwululira zomwe tinakupemphani, mwatiwululira maloto a mfumu.”


Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Yehova ndiye dzina lake lotchuka!


Koma inu muyenera kubwerera kwa Mulungu wanu; pitirizani chikondi ndi chiweruzo cholungama, ndipo muzidikira Mulungu wanu nthawi zonse.


Munthu uja ananyoza dzina la Yehova ndi kulitemberera. Choncho anabwera naye kwa Mose. Dzina la amayi ake linali Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.


Mitundu yonse ya anthu itha kutsatira milungu yawo; ife tidzayenda mʼnjira za Yehova Mulungu wathu mpaka muyaya.


“Ine ndine Yehova, ndipo sindisintha. Choncho inu zidzukulu za Yakobo, simunawonongedwe.


‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo.”


Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, wamulemekeza mtumiki wake Yesu. Amene inu munamukana pamaso pa Pilato ndi kumupereka Iye kuti aphedwe, ngakhale kuti Pilato anafuna kuti amumasule.


‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.’ Mose ananjenjemera chifukwa cha mantha ndipo sanalimbe mtima kuyangʼananso.


Yehova Mulungu wa makolo anu wachulukitsa chiwerengero chanu ndipo wakudalitsani monga momwe analonjezera!


“Palibe ndi mmodzi yemwe mwa mʼbado woyipawu amene adzaona dziko labwino limene ndinalumbira kupatsa makolo anu,


Mverani inu Aisraeli, malangizo ndi malamulo amene ndikuphunzitseni. Muwatsatire kuti mukhale ndi moyo ndi kuti mulowe ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akukupatsani.


Mʼmalo mwake, iwo amafunitsitsa dziko labwino, ndilo lakumwamba. Nʼchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wawo, pakuti Iye anawalonjeza mudzi.


Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa