Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 3:14 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Mulungu anati kwa Mose, “NDINE AMENE NDILI. Izi ndi zimene ukanene kwa Aisraeli: ‘NDINE wandituma kwa inu.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

14 Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Mulungu adamuuza kuti, “Dzina langa ndine NDILIPO. Aisraelewo ukaŵauze kuti, NDILIPO wandituma kwa inu.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 3:14
21 Mawu Ofanana  

“Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu? Kodi ungafufuze malire a nzeru za Wamphamvuzonse?


Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando, mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo; dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.


Mapiri asanabadwe, musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse, kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.


Yehova ndi wankhondo; Yehova ndilo dzina lake.


Muzimumvera ndi kumvetsetsa zimene akunena. Musamuwukire chifukwa sadzakhululuka kuwukira kwanu, pakuti akuchita zimenezi mʼdzina langa.


Mose anati kwa Mulungu, “Ngati ndipita kwa Aisraeli ndi kukawawuza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ ndipo iwo nʼkukandifunsa kuti ‘Dzina lake ndi ndani?’ Tsono ine ndikawawuze chiyani?”


Mulungu anatinso kwa Mose, “Ine ndine Yehova.


Ndinaonekera kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo monga Mulungu Wamphamvuzonse, koma sindinawadziwitse dzina langa kuti ndine Yehova.


“Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo! Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense kapena matamando anga kwa mafano.


“Yehova Mfumu ndi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndine woyamba ndi wotsiriza; palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha.


Pakuti pamene awiri kapena atatu asonkhana pamodzi mʼdzina langa, Ine ndili nawo pomwepo.”


ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”


Ine ndinakuwuzani kuti mudzafera mʼmachimo anu ngati simukhulupirira kuti Ine Ndine. Ndithu inu mudzafera mʼmachimo anu.”


Choncho Yesu anati, “Inu mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziwa kuti Ine Ndine. Mudzadziwa kuti sindichita kalikonse pa Ine ndekha koma ndimayankhula zokhazo zimene Atate anandiphunzitsa.


Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuzani choonadi, Abrahamu asanabadwe, Ine Ndine!”


Pakuti ngakhale malonjezo a Mulungu atachuluka chotani, onsewo ndi “Inde” mwa Khristu. Kotero kuti mwa Iye, ife timati “Ameni” kuchitira Mulungu ulemu.


Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse.


Nditamuona ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa. Kenaka Iye anasanjika dzanja lake lamanja pa ine nati, “Usachite mantha. Ndine Woyamba ndi Wotsiriza.


Ndine Yohane, Kupita ku mipingo isanu ndi iwiri ya mʼchigawo cha Asiya. Chisomo ndi mtendere kwa inu, kuchokera kwa Iye amene ali, amene analipo ndi amene akubwera ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala patsogolo pa mpando wake waufumu,


“Ine ndine Alefa ndi Omega,” akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo “amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo.”


Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo chinali ndi maso ponseponse ndi mʼkati mwa mapiko momwe. Usana ndi usiku zimanena mosalekeza kuti, “Woyera, woyera, woyera ndi Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, amene munali, amene muli ndi amene mukubwera.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa