Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 28:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Uwawuze anthu onse aluso amene Ine ndawapatsa nzeru pa ntchito yosoka kuti apange zovala za Aaroni za pa mwambo womupatula, kuti iye anditumikire monga wansembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire Ine ntchito ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire Ine ntchito ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ulamule anthu onse aluso, onse amene ndaŵapatsa nzeru, kuti asoke zovala za Aroni zozivala pamene udzampatule kuti akhale wansembe wanga.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:3
16 Mawu Ofanana  

mwana wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali ndipo abambo ake anali a ku Turo, mʼmisiri wa mkuwa. Hiramu anali munthu wa luso lalikulu ndiponso wodziwa kupanga zinthu za mkuwa. Iye anabwera kwa Mfumu Solomoni ndi kugwira ntchito zonse zimene anamupatsa.


“Anthu onse aluso pakati panu abwere ndi kupanga zonse zimene Yehova walamula:


Mayi aliyense waluso analuka ndi manja ake ndi kubweretsa chomwe analuka cha mtundu wa mtambo, chapepo kapena chofiira kapena chofewa, chosalala.


Kenaka Mose anati kwa Aisraeli, “Taonani, Yehova wasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda,


ndipo wamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi:


Mulungu wawapatsa maluso osiyanasiyana, maluso ogoba, olemba ndondomeko, opeta zokometsera pa nsalu zamtundu wamtambo, zapepo ndi zofiira ndiponso zofewa zosalala ndi zoluka. Onsewa ndi amisiri a ntchito zamanja ndi zokonza ndondomeko.


Choncho Bezaleli, Oholiabu pamodzi ndi anthu aluso onse amene Yehova anawapatsa luso ndi nzeru zodziwira kupanga zofunika zonse zomangira malo opatulika, adzapanga zonse iwowo, monga momwe Yehova analamulira.”


Ndipo Mose anayitana Bezaleli ndi Oholiabu ndiponso munthu aliyense waluso amene Yehova anamupatsa luso ndiponso amene anali ndi mtima wofuna kugwira ntchito.


Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru, ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.


Mzimu wa Yehova udzakhala pa iye Mzimu wanzeru ndi wa kumvetsa zinthu, Mzimu wauphungu ndi wamphamvu, Mzimu wachidziwitso ndi wakuopa Yehova.


Ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemerero akupatseni mzimu wa nzeru ndi wa vumbulutso, kuti mumudziwe kwenikweni.


Tsono Yoswa, mwana wa Nuni anadzazidwa ndi mzimu wanzeru chifukwa nʼkuti Mose atamusanjika manja. Choncho Aisraeli anamumvera ndipo anachita zomwe Yehova analamula Mose.


Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa