Eksodo 28:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Umusokere mʼbale wako, Aaroni, zovala zopatulika kuti azioneka mwaulemerero ndi molemekezeka. Onani mutuwoBuku Lopatulika2 Ndipo usokere Aroni mbale wako zovala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo usokere Aroni mbale wako zovala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Umsokere mkulu wako Aroni zovala zopatulika, kuti aziwoneka wolemerera ndi wolemekezeka. Onani mutuwo |
Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni, nkhata ya maluwa yokongola mʼmalo mwa phulusa, ndiwapatse mafuta achikondwerero mʼmalo mwa kulira. Ndiwapatse chovala cha matamando mʼmalo mwa mtima wopsinjika. Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo, yoyidzala Yehova kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.