Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 28:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Aaroni mʼbale wako ndi ana ake aamuna, Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara uwapatule pakati pa Aisraeli. Abwere kwa iwe kuti anditumikire monga ansembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake amuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Aroni ndi ana ake aamuna apatulidwe pakati pa Aisraele ndipo abwere kwa iwe, kuti akhale ansembe onditumikira. Abwere Aroni pamodzi ndi ana ake Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:1
33 Mawu Ofanana  

Ana a Amramu: Aaroni ndi Mose. Aaroni ndi zidzukulu zake anapatulidwa kwamuyaya kuti azipereka zinthu zopatulika kwambiri monga nsembe pamaso pa Yehova, komanso kuti azitumikira pamaso pake ndi kumadalitsa anthu mʼdzina lake kwamuyaya.


Yohanani anabereka Azariya (uyu ndi amene anatumikira monga wansembe mʼNyumba ya Mulungu imene Solomoni anamanga mu Yerusalemu),


mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Elieli, mwana wa Towa,


Alevi anasiya malo awo owetera ziweto ndi katundu wawo, ndi kubwera ku Yuda ndi ku Yerusalemu chifukwa Yeroboamu ndi ana ake anawakana kukhala ansembe a Yehova.


Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova; Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.


Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake, Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake; iwo anayitana Yehova ndipo Iyeyo anawayankha.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Bwera ku phiri kuno kwa Yehova, iwe pamodzi ndi Aaroni, Nadabu, Abihu ndi akuluakulu a Israeli makumi asanu ndi awiri. Enanu mundipembedze muli chapatali.


Kenaka Mose pamodzi ndi Aaroni, Nadabu, Abihu ndi akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Israeli aja anakwera ku phiri,


Zovala zimenezi umuveke Aaroni, mʼbale wako ndi ana ake. Kenaka uwadzoze, uwapatse udindo ndi kuwapatula kuti anditumikire ngati ansembe anga.


“Pofuna kumupatula Aaroni ndi ana ake kuti akhale ansembe onditumikira Ine, uchite izi: Utenge ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa ziwiri zazimuna zopanda chilema.


“Tsono Ine ndidzapatula tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Ndidzapatulanso Aaroni pamodzi ndi ana ake kuti akhale ansembe anga onditumikira.


ndi nduwira. Kenaka umange malamba Aaroniyo pamodzi ndi ana ake ndi kuwaveka nduwira. Motero unsembe udzakhala wawo malingana ndi lamulo ili losatha. “Umu ndi mmene udzadzozere Aaroni ndi ana ake aamuna.


“Udzoze Aaroni ndi ana ake aamuna ndi kuwapatula kuti akhale ansembe onditumikira.


ndiponso zovala zonse zolukidwa, zovala zopatulika za Aaroni wansembe pamodzi ndi za ana ake, zovala pamene akutumikira monga ansembe,


zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.”


Aaroni anakwatira Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wa Nasoni ndipo Iye anabereka Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.


Ana a Aaroni, Nadabu ndi Abihu, aliyense anatenga chofukizira lubani chake nayikamo makala a moto ndi kuthiramo lubani. Iwo anapereka pamaso pa Yehova moto wachilendo, moto umene Yehova sanawalamule.


Mose anawuza Aaroni ndi ana ake otsalawo, Eliezara ndi Itamara kuti, “Tengani zopereka zachakudya zopanda yisiti zimene zatsala pa nsembe zopsereza za kwa Yehova ndipo muzidye pafupi ndi guwa pakuti ndi zopatulika kwambiri.


Zimenezi ndi chigawo cha Aaroni ndi ana ake chotapidwa pa zopereka kwa Yehova zoti zitenthedwe pa moto zimene zinaperekedwa pa tsiku limene anapatulidwa kuti akhale ansembe otumikira Yehova.


Yehova anawuza Mose kuti,


“Tenga Aaroni ndi ana ake, zovala zawo, mafuta wodzozera, ngʼombe yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, nkhosa ziwiri zazimuna ndi dengu la buledi wopanda yisiti,


Koma iwe wekha ndi ana ako aamuna muzitumikira ngati ansembe ndi zina zonse zokhudza pa guwa lansembe ndi za mʼkati mwa malo wopatulika kwambiri. Ndikukupatsani mphatso ya utumiki wa unsembe. Aliyense woyandikira malo wopatulika ayenera kuphedwa.


Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 74,600.


Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo).


Nthawi yogwira ntchito yotumikira ansembe a gulu la Zekariya, Zekariya ankatumikira ngati wansembe pamaso pa Mulungu,


Aisraeli anayenda kuchokera ku Beeroti Beni Yaakani mpaka ku Mosera. Kumeneko Aaroni anamwalira nayikidwa mʼmanda, ndipo mwana wake Eliezara anakhala wansembe mʼmalo mwake.


pakuti Yehova Mulungu wanu wawasankha iwowa ndi ana awo pakati pa mafuko anu onse kuti aziyimirira ndi kutumikira mʼdzina la Yehova nthawi zonse.


Ndipo ndinamusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti akhale wansembe wanga ndi kuti azipita pa guwa langa la nsembe, kufukiza Lubani ndi kuvala efodi pamaso panga. Ndinapatsa banja la abambo ako gawo la nsembe zonse zopsereza zimene Aisraeli amapereka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa